Ndandanda ya Mlungu wa October 20
MLUNGU WA OCTOBER 20
Nyimbo 109 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 15 ndime 1 mpaka 6, ndi bokosi patsamba 184 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Deuteronomo 7-10 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 9:15-29 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cifukwa Cake Zinali Zotheka Kuti Munthu Wangwilo Acimwe—rs tsa. 358 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: Tisamakaikile Zimene Yehova Wasankha—(Aroma 11:33, 1 Yoh. 4:8 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 116
Mph. 15: “Kufotokoza Zimene Timakhulupilila Zokhudza 1914.” Kukambilana. Pemphani omvela kuti akambepo pa funso lililonse lili ndi kadontho kakuda.
Mph. 15: Cida Cimene Cingatithandize Kufotokoza Zimene Timakhulupilila Zokhudza 1914. Yambani ndi citsanzo ca mphindi 7 coonetsa wofalitsa akugwilitsila nchito chati cimene cili pa tsamba 216 mʼbuku lakuti Zimene Baibo Limaphunzitsa. Wofalitsayo akuthandiza Phunzilo la Baibulo kuona mmene ulosi wolembedwa mu Danieli caputala 4 umagwilizanilana ndi Ufumu wa Mulungu. Pemphani omvela kufotokoza cifukwa cake citsanzoci ndi cothandiza. Tsilizani mwa kuŵelenga Chivumbulutso 12:10, 12. Ndiyeno, pemphani omvela kufotokoza cifukwa cake kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila mu 1914 kumatilimbikitsa kulalikila mwacangu.
Nyimbo 133 ndi Pemphelo