Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa October 27, 2014.
Malinga ndi Numeri 21:5, n’cifukwa ciani Aisiraeli anali kuŵilingula kwa Mulungu ndi kwa Mose? Ndi cenjezo lotani limene tipezapo? [Sept. 1, w99 8/15 mas. 26-27]
N’cifukwa ciani Yehova anakwiyila Balamu? (Num. 22:20-22) [Sept. 8, w04 8/1 tsa. 27 ndime 2]
3. Kodi lemba la Numeri 25:11 litiuza ciani za khalidwe la Pinihasi? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake? [Sept. 8, w04 8/1 tsa. 27 ndime 4]
Ndi m’njila ziti zimene Mose anationetsela citsanzo cabwino kwambili ca kudzicepetsa? (Num. 27:5, 15-18) [Sept. 15, w13 2/1 tsa. 5]
Kodi Yoswa ndi Kalebe anapelekela bwanji umboni wamphamvu woonetsa kuti anthu opanda ungwilo akhoza kuyenda m’njila za Mulungu ngakhale akumane ndi citsutso? (Num. 32:12) [Sept. 22, w93 11/15 tsa. 14 ndime 13]
Kodi kumvela kwa ana aakazi a Tselofekadi kukukhudza bwanji mmene Akristu osakwatila kapena osakwatiwa amaonela cikwati? (Num. 36:10-12) [Sept. 29, w08 2/15 mas. 4-5 ndime 10]
Kodi kudandaula ndi kulankhula mau oipa kunawabweletsela vuto lanji Aisiraeli, ndipo ife tiphunzilapo ciani pankhani imeneyi? (Deut. 1:26-28, 34, 35) [Oct. 6, w13 8/15 tsa. 11 ndime 7]
Pofuna kuti Aisiraeli adalitsidwe ndi kuti akhale ndi moyo wabwino m’Dziko Lolonjezedwa, kodi Yehova anawapatsa maudindo aŵili ati? (Deut. 4:9) [Oct. 13, w06 6/1 tsa. 29 ndime 15]
Kodi zinatheka bwanji kuti zovala za Aisiraeli zisathe ndiponso kuti mapazi ao asatupe paulendo wa m’chipululu? (Deut. 8:3, 4) [Oct. 20, w04 9/15 tsa. 26 ndime 1]
Tingagwilitsile nchito motani cilimbikitso cimene Aisiraeli anapatsidwa cakuti “amamatile” kwa Yehova? (Deut. 13:4, 6-9) [Oct. 27, w02 10/15 tsa. 16 ndime 14]