LEMBA LA MWEZI: “LALIKILA MAU. LALIKILA MODZIPELEKA.”—2 Tim. 4:2.
Mmene Tingakhalile Acangu pa Nchito Yolalikila
Kuti tikapulumuke pa mapeto a dongosolo lino loipa la zinthu, tiyenela kukhala acangu pa nchito yolalikila. Tingathe kuonjezela cangu cathu mwa kutsatila zikumbutso zotsatilazi:
Tiyenela kupemphela nthawi zonse kuti Ufumu wa Mulungu ubwele.—Mat. 6:10.
Tiyenela kuteteza mtima wathu mwa kuŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku.—Aheb. 3:12.
Tifunika kugwilitsila nchito nthawi yathu mwanzelu.—Aef. 5:15, 16; Afil. 1:10.
Tiyenela kukhala ndi diso “lolunjika pa cinthu cimodzi,” ndipo tisamatengeke ndi zilakolako za m’dzikoli.—Mat. 6:22, 25; 2 Tim. 4:10.
Tiyenela kukhala maso ndi achelu pamene maulosi a m’Baibulo akukwanilitsidwa. —Maliko 13:35-37.
Kukhala acangu kudzatilimbikitsa kudzipeleka ndi mtima wonse kuti titsilize nchito imene ikugwilidwabe.—Yoh. 4:34, 35.