Ndandanda ya Mlungu wa November 3
MLUNGU WA NOVEMBER 3
Nyimbo 79 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 15 ndime 13 mpaka 20 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Deuteronomo 14-18 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 15:16–16:8 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cifukwa Cake Tiyenela Kuzindikila Kuti Chimo N’loopsa—rs tsa. 359 ndime 2–tsa. 360 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Ndi Zifukwa Ziti za m’Malemba Zimene Zimacititsa Anthu Kusudzulana—lv tsa. 219-220 ndime 1 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 103
Mph. 10: Thandizani Acicepele Kukonzekela Ulaliki. Kukambilana. Onelelani vidiyo yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Let’s Go in Service. (Pitani pa jw.org, ndi kuona polemba kuti BIBLE TEACHINGS > CHILDREN.) Ngati n’zosatheka kuonelela vidiyo imeneyi, kapena ngati sipezeka m’cinenelo canu, citani citsanzo cacidule coonetsa kholo likuthandiza wacicepele kukonzekela kupita mu ulaliki. Funsani ana mafunso awa: Ndi angati a inu amene ali ndi cola ca mu ulaliki? Kodi m’cola canu muli ciani? Kodi cinthu coyambilila cimene Sofiya anaika m’cola cake cinali ciani? N’cianinso cina cimene iye anafunika? Pambuyo pakuti waika zonse zofunikila m’cola, ndi cinthu cofunika citi cimene Sofiya anacita ndi amai ake? Wacicepele acite citsanzo coonetsa akugaŵila magazini.
Mph. 10: Mmene Ena Agwilila Nchito Yolalikila Mau Mwacangu. Mkulu afunse mafunso ofalitsa aŵili kapena atatu amene asintha zinthu zina ndi zina pa ndandanda yao ndi colinga cakuti aonjezele utumiki kapena kucitako upainiya. Tsilizani mwa kufotokoza zimene mpingo wakonza za ulaliki wa kumunda ndi kulimbikitsa onse kuti akatengeko mbali mokwanila.
Mph. 10: Kodi Mwanola Motani Luso Lanu mu Ulaliki? Nkhani yokambilana yokambidwa ndi woyang’anila nchito. Pemphani omvela kuti afotokoze mmene nkhani zaposacedwapa za mutu wakuti, “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki,” zawathandizila kunola luso lao mu ulaliki. Tsilizani mwa kulimbikitsa onse kuti apitilize kugwilitsila nchito malingalilo a m’nkhani zimenezi kuti azilalikila mwacangu.
Nyimbo 100 ndi Pemphelo