Zilengezo
◼ Cogaŵila ca mu October: Magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! November ndi December: Gaŵilani buku la mutu wakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena gaŵilani kalikonse ka tumapepala twauthenga utu: Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?, Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?, Kodi Mavuto Adzathadi?, ndi kakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo? January: Gaŵilani kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu.
◼ Ndife osangalala kuti m’caka cautumiki cino mpaka mwezi wa June, mipingo yatsopano yokwana 96 inapangidwa, ndipo Nyumba za Ufumu zatsopano zoposa 32 zinamangidwa.
◼ Galamukani! ya Cikikaonde idzayamba kutuluka kamodzi pamwezi, kuyambila ndi ya November 2014.
◼ Tikuyamikilani cifukwa colemba lipoti la zimene munagaŵila mu ulaliki wakumunda. M’mwezi wa March tinagaŵila tumabuku ndi tumapepala twauthenga toposa 892,000, cimeneci ndi ciŵelengelo capamwamba kuposa kale lonse.
◼ Ndife okondwa kukudziŵitsani kuti buku lakuti Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu, tsopano likupezeka m’cinenelo ca Cimambwe-Lungu.