Ndandanda ya Mlungu wa November 24
MLUNGU WA NOVEMBER 24
Nyimbo 131 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 1 ndime 10 mpaka 17, ndi bokosi patsamba 14 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Deuteronomo 28-31 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 30:15–31:8 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Nyama Zili Ndi Moyo—rs tsa. 295 ndime 6–tsa. 296 ndime 5 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mkristu Ayenela Kulandila Mankhwala Opangidwa Kucokela ku Tuzigawo Twamagazi?—lv tsa. 215-217 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 47
Mph. 10: “Gwilitsilani Nchito Webusaiti Yathu mu Ulaliki—‘Kuyankha Mafunso a m’Baibulo.’” Kukambilana. Fotokozani mafunso ena amene ayankhidwa m’cigawo ici ca Webusaiti yathu. (Pitani pa jw.org, ndi kuona polemba kuti BIBLE TEACHINGS > BIBLE QUESTIONS ANSWERED.) Citani citsanzo cacidule pogwilitsila nchito mfundo imodzi mwa mfundo za m’nkhaniyi. Pemphani omvela kuti anene njila zina za mmene angagwilitsile nchito cigawo cimeneci mu ulaliki.
Mph. 10: “Sindimupezanso Panyumba!” Kukambilana. Kambilanani kufunika kolimbikila ngati mwininyumba sakupezekanso panyumba.—Mat. 28:19, 20; Maliko 4:14, 15; 1 Akor. 3:6.
Mph. 10: “Cida Catsopano Cofufuzila.” Nkhani. Fotokozani malangizo a pa kamutu kakuti, “Poyambila Kufufuza” opezeka m’mau oyamba a Buku Lofufuzila Nkhani. Fotokozaninso mbali zosiyanasiyana za cida catsopano cimeneci. Ndiyeno citani citsanzo cacidule coonetsa wofalitsa akulankhula yekha pogwilitsila nchito buku limeneli.
Nyimbo 69 ndi Pemphelo