Ndandanda ya Mlungu wa January 12
MLUNGU WA JANUARY 12
Nyimbo 114 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 3 ndime 19 mpaka 21, bokosi pa tsa. 34 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Yoswa 21-24 (Mph. 8)
Na. 1: Yoswa 24:14-21 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mfumu Ahazi—Mutu: Mulungu Amadana ndi Munthu Amene Amalambila Mafano—w10 9/1 tsa. 14 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Yehova ndi Mlengi Wamphamvuyonse—igw-CIN tsa. 2 ndime 4–tsa. 3 ndime 1 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: ‘Tumikilani Ambuye monga kapolo, modzicepetsa kwambili.’—Machitidwe 20:19.
Nyimbo 61
Mph. 10: Tumikilani Ambuye Monga Kapolo, Modzicepetsa Kwambili. Kukambilana. Ŵelengani Machitidwe 20:19. Pemphani omvela kuti anenepo pa mafunso awa: (1) Kodi mau akuti “kapolo” amatanthauza ciani? (2) Ndi njila zina ziti zimene tingatumikilile Ambuye, Yesu Kristu monga akapolo? (3) Kodi kudzicepetsa n’kutani? (4) Kodi kudzicepetsa kumatithandiza bwanji kukwanilitsa utumiki wathu?
Mph. 20: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Mwininyumba Wokwiya.” Kukambilana. Pambuyo pa makambilano, khalani ndi citsanzo ca mbali ziŵili. Citsanzo coyamba cionetse wofalitsa ayankha mwaukali mwininyumba amene walankhula naye mokwiya, ndipo caciŵili wofalitsa ayankha mofatsa. Tsilizani mwa kulimbikitsa onse kuyesetsa kucita zimene zili pakamutu kakuti “Yesani Kucita Izi Mwezi Uno.”
Nyimbo 76 ndi Pemphelo