Ndandanda ya Mlungu wa February 2
MLUNGU WA FEBRUARY 2
Nyimbo 109 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 4 ndime 19 mpaka 23, bokosi pa tsa. 45 (30 min.)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Oweruza 8-10 (Mph. 8)
Na. 1: Oweruza 8:13-27 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Ndani Analemba Baibulo?—igw tsa. 6 Ndime 1-5 (Mph. 5)
Na. 3: Andireya—Mutu: Anali Munthu Wamba Koma Wokhulupilika Ndiponso Wofikilika—w14 3/15 tsa. 3 ndime 3-tsa. 4 ndime 2 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: ‘Tumikilani Ambuye monga kapolo, modzicepetsa kwambili.’—Machitidwe 20:19.
Nyimbo 110
Mph. 10: Kugaŵila Magazini mu February. Nkhani yokambilana. Yambani ndi zitsanzo zoonetsa mmene tingagaŵilile magazini mwa kugwilitsila nchito maulaliki acitsanzo pa tsamba lino. Ndiyeno kambilanani mmene citsanzo ciliconse cinalili.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Tinacita Zotani? Nkhani yokambilana. Pemphani ofalitsa kuti afotokoze mmene apindulila pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti, “Kunola Luso mu Ulaliki —Kuyankha Mwininyumba Wokwiya.” Pemphani omvela kuti afotokoze zocitika zabwino za mu ulaliki.
Nyimbo yatsopano “Tipatseni Kulimba Mtima” ndi Pemphelo
Cikumbutso: Lizani nyimbo yatsopanoyo kamodzi, kenako mpingo uimbile pamodzi nyimboyo.