Ndandanda ya Mlungu wa February 16
MLUNGU WA FEBRUARY 16
Nyimbo 80 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu. 5 ndime 9-17 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Oweruza 15-18 (Mph. 8)
Na. 1: Oweruza 16:13-24 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi m’Baibulo Muli Uthenga Wotani?—igw-CIN tsa. 8 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: Apolo—Mutu: Anali Mphunzitsi Waluso, Wodzicepetsa ndi Wacangu—w13 4/15 tsa. 9 ndime 10-11 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Khalani “Odzipeleka pa Nchito Zabwino.”—Tito 2:14.
Nyimbo 92
Mph. 15: Konzekelani Kulengeza Uthenga Wabwino Modzipeleka. Kukambilana. N’cifukwa ciani poyamba kukonzekela ulaliki tiyenela kupemphela? (Sal. 143:10; Mac. 4:31) Kuonjezela pa pemphelo, tiyenelanso kucita ciani? (Ezara 7:10) Pambuyo pakuti tadzikonzekeletsa, tiyenelanso kucita ciani cokhudzana ndi zofalitsa ndiponso cola ca mu ulaliki? Kodi kukonzekela kuli ndi ubwino wotani? (Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008, tsa. 10, ndime 9.) Kodi mumakonzekela bwanji ulaliki? Wofalitsa acite citsanzo ca mmene amakonzekelela ulaliki pogwilitsila nchito tumapepala, magazini, kapena mabulosha amene afuna kugaŵila mu ulaliki. Iye tsopano atenga cola cake ca mu ulaliki ndipo akuonetsetsa kuti ciwiya cake cokhala ndi intaneti cili bwinobwino kuti akacigwilitsile nchito mu ulaliki. Gogomezelani kuti tonse tifunika kukonzekela bwino popita mu ulaliki.—2 Tim. 3:17.
Mph. 15: “M’Nyengo Ino ya Cikumbutso, Kodi Mudzatengela Kudzipeleka kwa Yehova ndi Yesu?” Mafunso ndi mayankho. Gaŵilani kapepala kamodzi kwa aliyense ndipo kambilanani zimene zili m’kapepalako. Citani citsanzo cacidule, mwa kugwilitsila nchito maulaliki acitsanzo patsamba 4.
Nyimbo 30 ndi Pemphelo