Ndandanda ya Mlungu wa March 30
MLUNGU WA MARCH 30
Nyimbo 57 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 7 ndime 9-17 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Samueli 14–15 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Samueli 14:36-45 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Balamu—Mutu: Mtima Wadyela Ungatipangitse Kucita Zinthu Zoipa—(lv nkhani 9 tsa. 97 ndime 2) (Mph. 5)
Na. 3: Kukwanilitsidwa kwa Maulosi a m’Baibulo Okhudza Masiku Otsiliza—igw-CIN tsa. 13 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: ‘Khalani Okonzeka Kugwila Nchito Iliyonse Yabwino.’—Tito 3:1.
Nyimbo 37
Mph. 15: Mavidiyo Ena a pa Webusaiti Yathu Amene Tingagwilitsile Nchito mu Ulaliki. Kukambilana. Yambani mwa kuonetsa vidiyo yakuti, Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji? Ndiyeno kambilanani mmene mungagwilitsile nchito vidiyo imeneyi mu ulaliki. Citaninso cimodzimodzi ndi vidiyo yakuti, N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? Phatikizanipo citsanzo. Ngati n’zosatheka kuonelela vidiyo, kambilanani nkhani yakuti “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki” imene ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2014, tsamba 1.
Mph. 15: “Gwilitsilani Nchito Kabuku Kakuti, Mfundo za m’Mau a Mulungu—Poyambitsa Makambilano.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvela kuti anene mmene angagwilitsile nchito kabuku kakuti, Mfundo za m’Mau a Mulungu mu ulaliki. Citani citsanzo.
Nyimbo 114 ndi Pemphelo