Zilengezo
◼ Zogaŵila za mu June: Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena kamodzi ka tumapepala twa uthenga utu: Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?, Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?, Kodi Mavuto adzathadi?, ndi kakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo? July ndi August: Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. September: Magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani!
◼ Mukagaŵila tumapepala twa uthenga kapena twa ciitano, kaya mwangosiya panyumba pamene simunapeze munthu muyenela kulemba pa danga la “timabuku” polemba lipoti lanu la utumiki wa kumunda kumapeto kwa mwezi. Ngati munthu waonetsa cidwi ndipo walandila cofalitsa ngakhale kapepala kauthenga muyenela kubwelelako n’colinga cokulitsa cidwi cake.
◼ Kuyambila ndi Nsanja ya Mlonda ya July 15, 2015, a Mambwe-Lungu azikhala ndi Nsanja ya Mlonda yophunzila. Ndipo azikhalanso ndi yogaŵila imene izituluka pakapita miyezi iŵili kuyambila ndi ya July-August 2015.
◼ Mipingo ikulimbikitsidwa kuoda makadi a DPA (Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala), tumakhadi twa ofalitsa osabatizika ndi twa ana. Mungagwitisile nchito fomu yoodelapo mabuku ya (S-14) kapena kupyolela pa www.jw.org. Sitizitumizilanso mipingo mafomu amenewa pa caka.