Ndandanda ya Mlungu wa October 5
MLUNGU WA OCTOBER 5
Nyimbo 13 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 16 ndime 10-17 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mbiri 1-4 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mbiri 1:28-42 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Eli—Mutu: Kulekelela Zoipa Kumanyozetsa Mulungu—(w10 10/1 tsa.15 ndime 6-8) (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mau Akuti “Okana Kristu” Amatanthauza Ciani? (Mph. 5)
Msonkhano ya Nchito:
Lemba la Mwezi: “Kucitila umboni mokwanila za uthenga wabwino.”—Machitidwe 20:24.
Nyimbo 82
Mph. 10: Kugaŵila Magazini mu October. Kukambilana. Yambani ndi zitsanzo ziŵili zoonetsa mmene tingagaŵile magazini pogwilitsila nchito maulaliki acitsanzo amene tapatsidwa. Ndiyeno kambilanani maulaliki onse acitsanzo.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Tinacita Zotani? Kukambilana. Pemphani omvela kuti afotokoze mmene anapindulila pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti, “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila m’Gawo la Malonda.” Ndiyeno apempheni kuti afotokoze zocitika zabwino za mu ulaliki.
Nyimbo 98 ndi Pemphelo