LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 10/15 tsa. 2
  • Mmene Tingaphunzitsile Ena Mowafika Pamtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingaphunzitsile Ena Mowafika Pamtima
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Yesetsani Kuwafika pa Mtima Omvela
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Khalani Wolimba Mtima ndi Wozindikila Monga Yesu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 10/15 tsa. 2

Mmene Tingaphunzitsile Ena Mowafika Pamtima

1. Kodi kaphunzitsidwe ka Yesu kanakhudza bwanji mitima ya omvela ake?

1 Yesu Kristu anali kuphunzitsa omvela ake mowafika pamtima. Panthawi ina, iye anafotokozela ophunzila ake Malemba momveka bwino cakuti mitima yao inali “kunthunthumila.” (Luka 24:32) Popeza kumvela Mulungu kuyenela kucokela pansi pa mtima, kodi tingathandize bwanji anthu amene timaphunzila nao Baibulo kusintha umoyo wao?—Aroma 6:17.

2. Kodi kukhala wozindikila kumathandiza bwanji kuti tiphunzitse ena mowafika pamtima?

2 Khalani Wozindikila: Kungouza anthu kuti ici n’cabwino kapena ici n’coipa sikungawathandize kusintha. Komanso, kuwaŵelengela malemba ambilimbili otsutsa cikhulupililo cao, kungawacititse kuleka kuphunzila nafe. Kuti tithandize munthu kucitapo kanthu, coyamba tiyenela kudziŵa cifukwa cake amakhulupilila zinthu zinazake. Kufunsa mafunso mwaluso kungamucititse kufotokoza zakukhosi kwake. (Miy. 20:5) Tikadziŵa zimenezo, tingasankhe lemba limene lingamufike pamtima. Conco, tifunika kumuonetsa cidwi ndipo tiyenela kukhala woleza mtima. (Miy. 25:15) Kumbukilani kuti anthu amapita patsogolo mwakuuzimu mosiyanasiyana. Lolani mzimu woyela wa Yehova kuti uwathandize kusintha maganizo ao ndi zocita zao.—Maliko 4:26-29.

3. Tingathandize bwanji anthu amene timaphunzitsa kukhala ndi makhalidwe abwino?

3 Athandizeni Kukhala ndi Makhalidwe Abwino: Kuŵelenga nkhani za m’Baibulo zimene zikufotokoza ubwino ndi cikondi ca Yehova, kungathandize ophunzila kukhala ndi makhalidwe abwino. Tingaŵelenge malemba monga Salimo 139:1-4, ndi Luka 12:6, 7 kuti tiwaonetse cikondi cacikulu cimene Mulungu ali naco pa ife. Ngati anthu ayamikila kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova mocokela pansi pamtima, io adzam’konda kwambili Mulungu, ndipo adzakhala ofunitsitsa kudzipeleka kwa iye. (Aroma 5:6-8; 1 Yoh. 4:19) Cinanso, akadziŵa kuti zocita zao zimakhudza Yehova, adzalimbikitsidwa kucita zinthu zimene zimakondweletsa Mulungu ndi kum’lemekeza.—Sal. 78:40, 41; Miy. 23:15.

4. Tingalemekeze bwanji ufulu wosankha wa anthu amene timaphunzitsa mu ulaliki?

4 Yehova sakakamiza aliyense kumvela malamulo ake. M’malo mwake, amapempha anthu mwa kuwaonetsa ubwino wotsatila malangizo ake. (Yes. 48:17, 18) Tikamaphunzitsa ena mowafika pamtima ndi kuwathandiza kupanga okha cosankha, timatengela Yehova. Iwo akatsimikiza mtima kusintha umoyo wao, zotsatilapo zake zimakhala zabwino. (Aroma 12:2) Komanso amayandikila kwambili Yehova, “amene amayesa mtima.”—Miy. 17:3.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani