Ndandanda ya Mlungu wa October 26
MLUNGU WA OCTOBER 26
Nyimbo 15 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
ia mutu 1 ndime 1-13 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mbiri 12-15 (Mph. 8)
Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Khalani “ozikika mozama” ndi ‘okhazikika m’cikhulupililo.’—Akol. 2:6, 7.
Nyimbo 120
Mph. 10: Zogaŵila mu November. Kukambilana. Limbikitsani onse kugaŵila tumapepala twauthenga ndi buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa. Kambilanani mwacidule mfundo zothandiza za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2014 pa mutu wakuti“ “Tumapepala Twauthenga Twatsopano Topangidwa Mosangalatsa.” Citani citsanzo ca ulaliki umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu.
Mph. 20: “Kodi Mau a Mulungu Amagwila Nchito pa Umoyo Wanu?” Nkhani. Mukakamba mau oyamba acidule, lizani seŵelo la m’Baibulo la mau okha lopezeka pa jw.org kapena la pa CD lakuti “Musataye Mtima Pamene Yehova Akuongolelani!” Fotokozani mmene kusinkhasinkha Mau a Mulungu kungatithandizile kupeza mfundo zofunika kugwilitsila nchito paumoyo wathu. Malizani mwa kulimbikitsa onse kuti azimvetsela maseŵelo a m’Baibulo a mau okha opezeka pa jw.org.
Nyimbo 113 ndi Pemphelo