Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki kuyambila mlungu wa October 26, 2015.
Kodi nkhani yopezeka pa 2 Mafumu 13:18, 19 ikuonetsa bwanji kufunika kocita khama potumikila Mulungu? [Sept. 7, w10 4/15 tsa. 26 ndime 11]
Ndani anali kulamulila mu Israeli pamene Yona anali mneneli? Nanga tingaphunzile ciani pa utumiki wa Yona tikaona zimene zili pa 2 Mafumu 14:23-25? [Sept. 7, w09 1/1 tsa. 25 ndime 4]
Kodi Ahazi anaonetsa bwanji kuti sanakhulupilile mau amene Mulungu anakamba kudzela mwa mneneli Yesaya? Nanga tingadzifunse funso liti tisanapange zosankha zikuluzikulu? (2 Maf. 16:7) [Sept. 14, w13 11/15 tsa. 17 ndime 5]
Kodi Rabisake anagwilitsila nchito njila iti potsutsa anthu a Mulungu imenenso anthu otsutsa masiku ano amaigwilitsila nchito? Nanga ndi khalidwe liti limene lingatithandize kukana mabodza a anthu otsutsa? (2 Maf. 18:22, 25) [Sept. 14, w10 7/15 tsa. 13 ndime 3-4]
Kodi citsanzo ca Yosiya ca kudzicepetsa, cingatithandize bwanji kupindula tikamaŵelenga ndi kuphunzila Baibulo? (2 Maf. 22:19, 20) [Sept. 21, w00 3/1 tsa. 30 ndime 2]
Kodi zinthu zakale zimene zinapezeka zikutsimikizila bwanji kuti mafumu aŵili ochulidwa pa 2 Mafumu 25:27-30 analikodi? [Sept. 28, w12 6/1 tsa. 5 ndime 2-3]
Ndi zinthu zitatu ziti zimene Yabezi anapempha Yehova, ndipo zikutiphunzitsa ciani pankhani ya pemphelo? (1 Mbiri 4:9,10) [Oct. 5, w10 10/1 tsa. 23]
Kodi zotsatilapo za nkhondo yochulidwa pa 1 Mbiri 5:18-22, zingatilimbikitse bwanji kupitiliza kumenya nkhondo ya kuuzimu? [Oct. 12, w05 10/1 tsa. 9 ndime 7]
N’ciani cinathandiza Davide kumvetsa ndi kulemekeza mfundo ya m’lamulo la Yehova la kupatulika kwa magazi? Nanga citsanzo cake cingatilimbikitse kucita ciani? (1 Mbiri 11:17-19) [Oct. 19, w12 11/15 mas. 6-7 ndime 12-14]
Kodi Davide sanacite ciani pamene anali kusamutsila likasa lapangano ku Yerusalemu? Nanga tingaphunzilepo ciani pankhaniyi? (1 Mbiri 15:13) [Oct. 26, w03 5/1 mas. 10-11 ndime 11-13]