Kodi Mau a Mulungu Amagwila Nchito pa Umoyo Wanu?
Kuŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku kungatithandize kukhala “ozikika mozama” ndi ‘okhazikika m’cikhulupililo.’ (Akol. 2:6, 7) Koma kuti Mau a Yehova azigwila nchito pa umoyo wathu, tifunika kuwasinkhasinkha ndi kucita zimene taphunzila. (Aheb. 4:12; Yak. 1:22-25) Lemba la Yoswa 1:8, limachula mbali zitatu zothandiza tikamaŵelenga Baibulo: (1) Kuŵelenga Mau a Mulungu “usana ndi usiku.” (2) “Kusinkhasinkha,” kutanthauza kuti tiyenela kuŵelenga paliwilo loyenela n’colinga cakuti tisinkhesinkhe ndi kuona zocitikazo m’maganizo mwathu. (3) Kutsimikiza mtima ‘kutsatila zonse zolembedwamo.’ Kucita zimenezi kudzatithandiza ‘kukhala ndi moyo wopambana.’ Kudzatithandizanso ‘kucita zinthu mwanzelu’ tsiku lililonse.