LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 September masa. 2-7
  • “Muzicita Zimene Mawu Amanena”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Muzicita Zimene Mawu Amanena”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUZIPATULA NTHAWI YOŴELENGA MAWU A MULUNGU
  • MUZISINKHASINKHA ZIMENE MWAŴELENGA
  • DZIIKILENI ZOLINGA ZIMENE MUKHOZA KUZIKWANILITSA
  • LOLANI MAWU A MULUNGU “KUGWILA NCHITO MWA INU”
  • Kufuna-funa Nzelu mwa Kuŵelenga Baibo Tsiku Lililonse
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Mmene Tingaonjezele Cimwemwe Cathu mu Ulaliki
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 September masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZILA 36

NYIMBO 89 Mvela Udalitsike

“Muzicita Zimene Mawu Amanena”

“Muzicita zimene mawu amanena, osati kungomva cabe.”​—YAK. 1:22.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Nkhani ino itithandiza kukulitsa cifuno cathu coŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, kuwasinkhasinkha, na kucita zimene tikuŵelengazo.

1-2. N’cifukwa ciyani atumiki a Yehova ali acimwemwe? (Yakobo 1:22-25)

YEHOVA na Mwana wake wokondeka amafuna kuti tizikhala okondwela. Wolemba Salimo 119:2 anati: “Osangalala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake, amene amamufunafuna ndi mtima wawo wonse.” Nayenso Yesu anawonjezela pa mfundoyi pomwe anati: “Osangalala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu nʼkuwasunga!”​—Luka 11:28.

2 Alambili a Yehova ni anthu acimwemwe. Cifukwa ciyani? Tili na zifukwa zambili, koma cifukwa cacikulu n’cakuti timaŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, ndipo timayesetsa kucita zimene taŵelenga.​—Ŵelengani Yakobo 1:22-25.

3. Timapindula bwanji tikamacita zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu?

3 Timapeza mapindu ambili ngati timacita “zimene mawu amanena.” Mwa citsanzo, tikacita zimene taŵelenga m’Mawu a Mulungu, timakondweletsa Yehova. Kucita zimenezi kumatibweletsela cimwemwe. (Mlal. 12:13) Tikamacita zimene timaŵelenga m’Mawu ouzilidwa a Mulungu, timakhala paubale wolimba na a m’banja lathu komanso okhulupilila anzathu. Mwina mwaona kuti mfundoyi ni yoona pa umoyo wanu. Kuwonjezela apo, timapewa mavuto ambili amene anthu omwe satsatila mfundo za Yehova amakumana nawo. Zili monga anakambila Mfumu Davide. Davide m’nyimbo yake atachula za cilamulo ca Yehova na zigamulo zake, ananena kuti: “Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.”​—Sal. 19:7-11.

4. N’cifukwa ciyani kungakhale kovuta kucita zimene Mawu a Mulungu amakamba?

4 Kuti tizicita zimene Mawu a Mulungu amakamba, tiyenela kuŵelenga Baibo kuti timvetse zimene Yehova afuna kuti tizicita. Koma kupeza nthawi yoŵelenga Baibo kumakhala kovuta cifukwa tili na zocita zambili. Conco timafunika kucita kupatula nthawi yoŵelenga. Tiyeni tikambilane zimene tingacite kuti tiziŵelenga Baibo tsiku lililonse. Tionenso zimene zingatithandize kuti tiziganizila zimene taŵelenga na kuona zimene tingacite kuti tiziziseŵenzetsa pa umoyo wathu.

MUZIPATULA NTHAWI YOŴELENGA MAWU A MULUNGU

5. Ni zinthu ziti zimene zimatitengela nthawi?

5 Ambili mwa anthu a Yehova ni otangwanika kwambili. Timathela nthawi yoculuka kusamalila maudindo amene Malemba amati ni ofunika kwambili. Mwa citsanzo, ambili a ife timagwila nchito yakuthupi kuti tipeze zofunika pa umoyo, komanso kuti tisamalile mabanja athu. (1 Tim. 5:8) Akhristu ambili amasamalila acibale awo, odwala, kapena okalamba. Ndipo aliyense wa ife ayenela kusamalila thanzi lake. Zimenezi zimafuna nthawi. Kuwonjezela pa maudindo amenewa, tilinso na zocita zina zofunika mumpingo. Ndipo udindo wina wofunika umene tili nawo, ni kutengako mbali mokangalika pa nchito yolalikila. Popeza munthu aliyense ali na zocita zambili, mungapeze bwanji nthawi yoti muziŵelenga Baibo tsiku lililonse, kusinkhasinkha, na kucita zimene mwaŵelenga?

6. Tingacite ciyani kuti tiziŵelenga Baibo tsiku lililonse? (Onaninso cithunzi.)

6 Kwa ife Akhristu, kuŵelenga Baibo ni cimodzi mwa zinthu “zofunika kwambili.” Conco tifunika kuyesetsa kupeza nthawi yoŵelenga Baibo. (Afil. 1:10) Ponena za munthu wacimwemwe, salimo yoyambilila imati: “Amakonda kwambili cilamulo ca Yehova, ndipo amaŵelenga ndi kuganizila mozama cilamuloco masana ndi usiku.” (Sal. 1:1, 2) Izi zionetsa kuti tiyenela kumapatula nthawi yoŵelenga Baibo. Kodi nthawi yabwino yoŵelenga Baibo ni iti? Aliyense angasankhe nthawi imene ingamukomele. Koma cofunika kwambili ni kusankha nthawi imene ingakuloleni kuti muziŵelenga Baibo tsiku lililonse. M’bale wina dzina lake Victor anati: “Ine nimakonda kuŵelenga Baibo m’mamawa. Ngakhale kuti sinikonda kuuka m’mamawa, nimaona kuti nthawi imeneyi ni yabwino ngako cifukwa sipakhala zosokoneza zambili. Sinikhala na zambili m’maganizo, moti nimatha kuika maganizo anga pa zimene nikuŵelenga.” N’kutheka kuti inunso mumaona conco. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nthawi yabwino kwambili kwa ine yoŵelenga Baibo ni iti?’

Mlongo akuŵelenga Baibo pamene mwana wake wagona m’cipinda.

Kodi nthawi yabwino kwa inu imene mungathe kuŵelenga Baibo tsiku lililonse ni iti? (Onani ndime 6)


MUZISINKHASINKHA ZIMENE MWAŴELENGA

7-8. N’ciyani cingatilepheletse kupindula mokwanila na zimene timaŵelenga? Fotokozani citsanzo.

7 N’zoona kuti ndandanda yoŵelenga Baibo tingakhale nayo. Komabe tingamaŵelenge zambili, koma osamvetsa zimene tikuŵelengazo. Kodi munaŵelengapo cinacake, koma posapita nthawi munaiŵala zimene munaŵelengazo? Tonse zinaticitikilapo zimenezi. Ndipo zingacitikenso pamene tikuŵelenga Baibo. Mwina munadziikila colinga coŵelenga macaputala angapo a m’Baibo tsiku lililonse. Colinga cimeneci n’cabwino kwambili. Tiyenela kudziikila zolinga na kuyesetsa kuzikwanilitsa. (1 Akor. 9:26) Komabe, kuŵelenga Baibo ni ciyambi cabe. Pali zina zimene tiyenela kucita kuti tipindule mokwanila tikamaŵelenga Mawu a Mulungu.

8 Kuti timvetsetse mfundoyi, tiyelekeze motele: Madzi ni ofunika kuti zomela zikule. Koma mvula ikagwa yambili m’kanthawi kocepa, madzi oculuka amangopitilila ndipo saloŵa m’nthaka. Zimakhala bwino mvula ikamagwa pang’ono-pang’ono, cifukwa madzi amaloŵa bwino m’nthaka ndipo zomela zimakula bwino. Mofananamo, tiyenela kupewa kuŵelenga Baibo mothamanga, moti n’kulephela kusinkhasinkha zimene taŵelenga, kuzikumbukila, komanso kuzigwilitsa nchito.​—Yak. 1:24.

M’bale akuŵelenga Baibo. Zithunzi: 1. Mvula ikugwa yaikulu ndipo zimenezi zikucititsa kuti zomela zisakule bwino. 2. Mvula ikugwa pang’ono-pang’ono ndipo zimenezi zikucititsa kuti zomela zikule bwino.

Mvula ikagwa, pamafunika nthawi kuti madzi aloŵe pansi kuti zomela ziseŵenzetse madziwo. Mofananamo, timafunikila nthawi yokwanila kuti tiŵelenge na kucita zimene taŵelenga m’Mawu a Mulungu (Onani ndime 8)


9. Tiyenela kutani tikazindikila kuti timaŵelenga Baibo mothamanga?

9 Kodi nthawi zina mumaona kuti mumaŵelenga Baibo mothamanga? Kodi muyenela kucita ciyani mukazindikila zimenezi? Ŵelengani modekha kuti muzikhala na nthawi yosinkhasinkha zimene mukuŵelengazo, komanso kuti muzitha kukumbukila zimene munali kuŵelenga. Kusinkhasinkha sikovuta. Ngati kwa inu kusinkhasinkha kukumveka kovuta, m’mawu ena tinganene kuti muziganizila zimene mukuŵelenga. Mungawonjezeleko nthawi imene mumathela poŵelenga kuti mukhale na mpata woganizilapo, kapena kuti kusinkhasinkha. Mwinanso mungamaŵelenge mavesi ocepelapo kuti muzitsalako na nthawi yoganizila zimene mwaŵelenga. Victor amene tamuchula uja anati, “Pamene niŵelenga Baibo, sinimaŵelenga zoculuka. Nthawi zina nimaŵelenga caputala cimodzi cabe. Cifukwa cakuti nimaŵelenga m’mawa, nimakhala na nthawi yosinkhasinkha zimene naŵelengazo kwa tsiku lonse.” Kaya mumaseŵenzetsa njila yotani poŵelenga, cofunika kwambili ni kuŵelenga pa liŵilo limene lingakuloleni kuti muzipindula na zimene mwaŵelengazo.​—Sal. 119:97; onani bokosi lakuti “Mafunso Amene Mungaganizilepo.”

Mafunso Amene Mungaganizilepo

Kuti mupindule kwambili poŵelenga Baibo, ganizilani funso limodzi kapena angapo pa mafunso awa:

  • Kodi izi ziniphunzitsa ciyani ponena za Yehova?

  • Kodi Lembali linithandiza bwanji kumvetsa uthenga wonse wa m’Baibo?

  • Kodi ningaseŵenzetse bwanji zimene naŵelengazi pa umoyo wanga?

  • Kodi mavesiwa ningathandize nawo bwanji anthu ena?

10. Pelekani citsanzo ca mmene tingagwilitsile nchito zimene taŵelenga. (1 Atesalonika 5:17, 18)

10 Kaya musankha nthawi yanji yoŵelenga Baibo, komanso kuculuka kwa nthawi yoŵelenga, muziona mmene mungagwilitsile nchito zimene mwaŵelenga. Pamene mukuŵelenga Mawu a Mulungu, muzidzifunsa kuti, ‘Ningaseŵenzetse bwanji zimene naŵelengazi pali pano kapena m’tsogolo?’ Tiyelekeze kuti mwaŵelenga 1 Atesalonika 5:17, 18. (Ŵelengani.) Mutaŵelenga mavesi aŵili amenewa, mungadzifunse ngati mumapemphela pafupi-pafupi, komanso ngati mumapeleka mapemphelo ocokela pansi pa mtima. Kuwonjezela apo, mungaganizile zinthu zimene mumayamikila. Mwina mungaganizile kuti muyamikile Yehova pa zinthu zitatu. Ngakhale mutacita zimenezi kwa mphindi zocepa, kudzakuthandizani kuti mukhale munthu womva Mawu a Mulungu na kuwacita. Ganizilani mmene mungapindulile mukamacita zimenezi tsiku lililonse pamene muŵelenga Baibo! Kucita izi kudzakuthandizani kuti muzicita zimene Mawu a Mulungu amanena. Bwanji ngati zioneka kuti muli na zambili zimene muyenela kuwongolela?

DZIIKILENI ZOLINGA ZIMENE MUKHOZA KUZIKWANILITSA

11. N’ciyani cingakucititseni kukhala na ulesi woŵelenga Baibo nthawi zina? Pelekani citsanzo.

11 Nthawi zina mungacite ulesi kuŵelenga Baibo mukaona kuti pali zambili zimene mufunika kuwongolela. Ganizilani citsanzo ici. Tinene kuti pa tsiku loyamba la kuŵelenga Baibo kwanu, mwapeza uphungu wakuti sitiyenela kucita zinthu mokondela. (Yak. 2:1-8) Ndipo mwaona kuti mufunika kusintha mmene mumacitila zinthu na ena, moti mwatsimikiza mtima kucita zimenezo. Cimeneco n’colinga cabwino kwambili! Pa tsiku laciŵili, mukuŵelenga mavesi amene aonetsa kufunika kolamulila lilime lathu. (Yak. 3:1-12) Zimenezi zakupangitsani kuzindikila kuti nthawi zina mumakamba zinthu zosalimbikitsa. Conco mwatsimikiza mtima kuti muzikamba zinthu zolimbikitsa. Pamene mukuŵelenga Baibo pa tsiku lacitatu, mukupeza cenjezo lakuti sitiyenela kukhala bwenzi la dziko. (Yak. 4:4-12) Conco mukuzindikila kuti muyenela kukhala wosamala na zimene mumaŵelenga, kuonelela, komanso kumvetsela. Podzafika tsiku lacinayi, mungayambe kuona kuti pali zambili zimene mufunika kuwongolela, moti mukucita ulesi.

12. N’cifukwa ciyani sitiyenela kulefuka pamene tikuŵelenga Baibo tikazindikila kuti pali zinthu zimene tifunika kuwongolela? (Onaninso mawu a m’munsi.)

12 Musalefuke mukazindikila kuti pali zambili zimene mufunika kuwongolela. Mukazindikila kuti mufunika kuwongolela zinazake, zimaonetsa kuti ndinu munthu wodzicepetsa, komanso kuti muli na zolinga zabwino. Munthu wodzicepetsa komanso woona mtima, amaŵelenga Malemba na colinga coona pamene afunika kuwongolela.a Ndipo kumbukilani kuti tifunika kupitiliza kuvala “umunthu watsopano.” (Akol. 3:10) N’ciyani cingakuthandizeni kupitiliza kucita zimene Mawu a Mulungu amanena?

13. Mungadziikile bwanji zolinga zing’ono-zing’ono zimene mukhoza kuzikwanilitsa? (Onaninso cithunzi.)

13 M’malo mofuna kucita zonse zimene mwaŵelenga pa nthawi imodzi, dziikileni zolinga zing’ono-zing’ono zimene mukhoza kuzikwanilitsa. (Miy. 11:2) Yesani kucita izi: Lembani zinthu zimene mufunika kuwongolela. Kenako sankhani cimodzi kapena ziŵili pa zinthuzo zimene mukufuna kuwongolela coyamba, na kusiya zinazo kuti mudzazicite m’tsogolo. Mungayambile na zinthu ziti?

Zithunzi: 1. Pamene mlongo akucita phunzilo la munthu mwini, akulemba pa pepala colinga cimene afuna kucikwanilitsa. 2. Akuika pepala limenelo pa bolodi. Pa pepala limenelo pali mawu akuti: “Mlungu uno, kudekha, Miyambo 15:1.”

M’malo mofuna kucita zonse zimene mwaŵelenga m’Baibo pa nthawi imodzi, dziikileni zolinga zing’ono-zing’ono zimene mungakwanilitse. Mwina mungayambe na cinthu cimodzi kapena ziŵili (Onani ndime 13-14)


14. Ni zolinga ziti zimene mungazikwanilitse coyamba?

14 Mungayambile na colinga cimene muona kuti n’cosavuta kucikwanilitsa. Kapena mungayambe na zinthu zimene muona kuti ni zofunikiladi kuwongolela. Mukasankha colinga cimene mukufuna kucikwanilitsa, fufuzani mu zofalitsa zathu. Mwina mungaseŵenzetse Laibulale ya pa Intaneti ya Watchtower, kapena Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Pemphelelani colinga cimeneco. M’pempheni Yehova kuti akupatseni mtima “wofuna kucita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zocitila zinthuzo.” (Afil. 2:13) Kenako, gwilitsani nchito zimene mwaphunzila. Mukakwanitsa kukulitsa khalidwe lina la Cikhristu, mudzalimbikitsidwa kupitiliza kuwongolela. Ndipo izi zidzapangitsa kuti cikhale cosavuta kuwongolela pa mbali zina.

LOLANI MAWU A MULUNGU “KUGWILA NCHITO MWA INU”

15. Kodi anthu a Yehova amasiyana bwanji na anthu ambili amene amaŵelenga Baibo? (1 Atesalonika 2:13)

15 Anthu ena amakamba kuti aiŵelengapo Baibo yonse nthawi zambili. Koma kodi amakhulupililadi zimene imaphunzitsa? Ndipo kodi amacita zimene amaŵelenga, komanso kuilola kuti iziwatsogolela pa umoyo wawo? Ambili satelo. Koma anthu a Yehova amacita mosiyana na anthu amenewo! Monga mmene Akhristu oyambilila anacitila, nafenso timaona Baibo mmene ililidi, “monga Mawu a Mulungu.” Kuwonjezela apo, timayesetsa kucita zimene taŵelenga m’Baibo.​—Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13.

16. N’ciyani cingatithandize kuti tizicita zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu?

16 Nthawi zina kumakhala kovuta kuŵelenga Mawu a Mulungu na kucita zimene timaŵelenga. Tingavutike kupeza nthawi yoŵelenga. Mwinanso tingamaŵelenge mothamanga kwambili, moti n’kulephela kumvetsa zimene tikuŵelengazo. Tingaonenso kuti tili na zambili zimene tifunika kuwongolela. Koma na thandizo la Yehova, mungakwanitse kugonjetsa vuto lina lililonse limene limakulepheletsani kuŵelenga, komanso kuseŵenzetsa zimene mukuŵelengazo. Tiyeni nthawi zonse tizilola Mulungu kutithandiza kukhala anthu amene amacita zimene Mawu amanena, osati amene amangomva n’kuiŵala. Mosakayikila, tikamapatula nthawi yoŵelenga Mawu a Mulungu na kucita zimene mawuwo amanena, tidzakhala acimwemwe.​—Yak. 1:25.

N’CIYANI CINGATITHANDIZE . . .

  • kupeza nthawi yoŵelenga Baibo tsiku lililonse?

  • kusinkhasinkha, kapena kuganizila zimene taŵelenga?

  • kucita zimene timaŵelenga?

NYIMBO 94 Tiyamikila Mau a Mulungu

a Onani vidiyo yakuti Zimene Acinyamata Anzanu Amakamba—Kuŵelenga Baibo pa jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani