LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 March tsa. 11
  • Kufuna-funa Nzelu mwa Kuŵelenga Baibo Tsiku Lililonse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kufuna-funa Nzelu mwa Kuŵelenga Baibo Tsiku Lililonse
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Lembani Mmene Mwapitila Patsogolo
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Mmene Tingaonjezele Cimwemwe Cathu mu Ulaliki
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 March tsa. 11

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kufuna-funa Nzelu mwa Kuŵelenga Baibo Tsiku Lililonse

Nzelu zocokela kwa Mulungu n’zamtengo wapatali mofanana na cuma cobisika. (Miy. 2:1-6) Nzelu zimatithandiza kupanga zisankho zabwino, kukhala oganiza bwino, komanso zimatiteteza. Conco, nzelu “ni cinthu cofunika kwambili.” (Miy. 4:5-7) Kulimbikila n’kofunika kuti tipeze cuma cauzimu cobisika cimene cili m’Mawu a Mulungu. Tingayambe kucita izi mwa kumaŵelenga Mawu a Mulungu “usana ndi usiku,” kapena kuti tsiku lililonse. (Yos. 1:8) Onani zina zimene zingatithandize kuti tiziŵelenga Baibo nthawi zonse, komanso kuti tizisangalala poiŵelenga.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ACICEPELE PHUNZILANI KUKONDA MAWU A MULUNGU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

Ni zovuta zotani zimene acinyamatawa anakumana nazo pamene anali kuyesetsa kuŵelenga Baibo tsiku lililonse? Nanga n’ciyani cinawathandiza?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Acicepele Phunzilani Kukonda Mawu a Mulungu.” Melanie.

    Melanie

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Acicepele Phunzilani Kukonda Mawu a Mulungu.” Samuel.

    Samuel

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Acicepele Phunzilani Kukonda Mawu a Mulungu.” Celine.

    Celine

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti “Acicepele Phunzilani Kukonda Mawu a Mulungu.” Raphaello.

    Raphaello

NDANDANDA YANGA YA KUŴELENGA BAIBO:

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani