Ndandanda ya Mlungu wa November 2
MLUNGU WA NOVEMBER 2
Nyimbo 52 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
ia mutu 1 ndime 14-27, ndi kubwelelamo tsa. 16 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mbiri 16–20 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mbiri 17:15-27 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Likasa la Pangano Linali Ciani? (Mph. 5)
Na. 3: Elifazi—Mutu: Yehova Amadana ndi Lilime Lonama—w05 9/15 tsa. 26 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Khalani “ozikika mozama” ndi ‘okhazikika m’cikhulupililo.’—Akol. 2:6, 7.
Nyimbo 91
Mph. 10: Kugaŵila Magazini mu November. Kukambilana. Yambani mwa kucita zitsanzo ziŵili pogwilitsila nchito maulaliki acitsanzo. Ndiyeno, kambilanani maulaliki onse acitsanzo kucokela kuciyambi mpaka kumapeto.
Mph. 10: Zosoŵa za Pampingo.
Mph. 10: Tinacita Zotani? Kukambilana. Pemphani omvela kuti akambe mmene anapindulila pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Thandizani Ophunzila Kukhala ndi Cizolowezi Cabwino Cophunzila Baibulo.” Ndiyeno, pemphani omvela kuti afotokoze zocitika zabwino za mu ulaliki.
Nyimbo 140 ndi Pemphelo
Cikumbutso: Lizani nyimbo yatsopanoyo kamodzi, kenako mpingo uimbile pamodzi nyimboyo.