LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 12/15 tsa. 3
  • Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 12/15 tsa. 3

Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki

Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa December 28, 2015. Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizitha kufufuza mfundozo pokonzekela.

  1. Kodi Davide anali kucitila nkhanza anthu amene anawagwila kunkhondo, monga mmene ena amaganizila akaŵelenga 1 Mbiri 20:3? [Nov. 2, w05 2/15 tsa. 27]

  2. N’ciani cinathandiza Davide kuonetsa mzimu woolowa manja? Nanga n’ciani cingatithandize kuonetsa mzimu wotelo? (1 Mbiri 22:5) [Nov. 9, w05 10/1 tsa. 11 ndime 7]

  3. Kodi Davide anatanthauza ciani pamene anauza Solomo kuti: “Dziŵa Mulungu wa bambo wako”? (1 Mbiri 28:9) [Nov. 16, w10 11/1 tsa. 25 ndime 3, 7]

  4. Kodi pemphelo la Solomo lopezeka pa 2 Mbiri 1:10 linaonetsa ciani za iye? Nanga tingaphunzile ciani tikamaganizila zopeleka pemphelo kwa Yehova? (2 Mbiri 1:11, 12) [Nov. 23, w05 12/1 tsa. 19 ndime 6]

  5. Malinga ndi lemba la 2 Mbiri 6:29, 30, kodi Yehova angathe kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kumuuza zakukhosi kwathu? (Sal. 55:22) [Nov. 30, w10 12/1 tsa. 11 ndime 7]

  6. Kodi Asa anadalila ndani kumuthandiza kugonjetsa adani ake amene anali ambili? Nanga ife tingakhale otsimikiza za ciani pa nkhondo yathu yakuuzimu? (2 Mbiri 14:11) [Dec. 7, w12 8/15 tsa 8 ndime 6–tsa. 9 ndime 1]

  7. Tikuphunzilapo ciani pa cikondi cimene Yehova anaonetsa Mfumu Yehosafati atacimwa? Nanga zimenezi ziyenela kukhudza bwanji mmene timaonela anthu ena? (2 Mbiri 19:3) [Dec. 14, w03 7/1 tsa 17 ndime 13; cl tsa. 245 ndime 12]

  8. N’cifukwa ciani tifunika kukhala ‘m’malo athu’ ndi ‘kuima cilili’ masiku ano? Nanga tingacite bwanji zimenezi? (2 Mbiri 20:17) [Dec. 21, w05 12/1 tsa. 21 ndime 3; w03 6/1 tsa 21 ndime 15-16]

  9. Ndi phunzilo lotani limene tingatengepo pa 2 Mbiri 21:20, yokhudza imfa ya Yehoramu? [Dec. 21, w98 11/15 tsa. 32 ndime 4]

  10. Malinga ndi 2 Mbiri 26:5, ndani analimbikitsa Uziya, mfumu yacinyamata? Nanga acinyamata angaphunzile ciani kwa Akristu okhwima mwakuuzimu mumpingo? [Dec. 28, w07 12/15 tsa. 10 ndime 2, 4]

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani