Zilengezo
◼ Zogaŵila mu December: Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena kamodzi mwa tumapepala twauthenga utu: Kodi Baibo mumaiona bwanji?, Kodi zinthu zidzakhala bwanji mtsogolo?, Kodi cofunika n’ciani kuti banja likhale lamtendele?, Kodi ndani maka-maka amene akulamulila dzikoli?, Kodi mavuto adzathadi?, ndi kakuti Kodi n’zoona kuti akufa angakhalenso ndi moyo? January ndi February: Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu March: Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani.
◼ Cikumbutso ca mu 2017 cidzacitika pa Ciŵili pa April 11, 2017.