Ndandanda ya Mlungu wa December 14
MLUNGU WA DECEMBER 14
Nyimbo 50 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
ia mutu 4 ndime 16-31, ndi kubwelelamo pa tsa. 41 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Mbiri 15-19 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Mbiri 16:1-9 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Dziko la Akasidi Linali Kuti, Nanga Akasidi Anali Ndani? (Mph. 5)
Na. 3: Esau—Mutu: Zosankha Zathu Zimaonetsa Kuti Timayamikila Zinthu Zopatulika—w13 5/15 tsa. 27-28 ndime 6-11 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”—Machitidwe 14:22.
Nyimbo 128
Mph.30: “Yendani mwa Cikhulupililo, Osati mwa Zooneka ndi Maso.” Mafunso ndi mayankho. Gwilitsani nchito mfundo za m’ndime yoyamba ndi yomaliza monga mau oyamba ndi omaliza. Ngati n’zosatheka kuonelela vidiyo, kambilanani mwa mafunso ndi mayankho nkhani yakuti “Yendani mwa Cikhulupililo, Osati mwa Zooneka ndi Maso,” mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2005 tsamba 16-20.
Nyimbo 133 ndi Pemphelo