CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | 2 MBIRI 29–32
Kulambila Koona Kumafuna Kugwila Nchito Mwakhama
Yopulinta
Hezekiya abwezeletsa kulambila koona molimba mtima
29:10-17
746-716 B.C.E.
Ulamulilo wa Hezekiya
NISANI 746 B.C.E.
Tsiku loyamba mpaka la 8: Kuyeletsa bwalo lamkati
Tsiku la 9 mpaka la 16: Kuyeletsa nyumba ya Yehova
Kuphimba macimo a Aisiraeli onse ndiponso kubwezeletsa kulambila koona zinayamba
740 B.C.E
Kugonjetsedwa kwa Mzinda wa Samariya
Hezekiya aitana anthu onse a mtima wabwino kuti adzalambile Mulungu
30:5, 6, 10-12
Asilikali othamanga anatumidwa kukapeleka makalata olengeza za Pasika m’madela onse a dzikolo kuyambila ku Beere-seba mpaka ku Dani
Anthu ena anali kunyoza, koma ambili analandila uthengawo mwacisangalalo