CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | 2 MBIRI 33–36
Yehova Amaona Munthu Wolapa ndi Mtima Wonse Kukhala Wamtengo Wapatali
Yopulinta
MANASE
Yehova analola kuti agwidwe ndi Asuri ndipo anapita naye ku Babulo m’matangadza
ULAMULILO WAKE ASANATENGEDWE KU UKAPOLO
Anamangila milungu yonama maguwa ansembe
Anapeleka ana ake nsembe
Anakhetsa magazi a anthu osalakwa
Analimbikitsa anthu onse kucita zamatsenga
ULAMULILO WAKE ATAMASULIDWA
Anadzicepetsa kwambili
Anapemphela kwa Yehova; ndipo anapeleka nsembe
Anacotsa maguwa a nsembe a milungu yonama
Analimbikitsa anthu onse kutumikila Yehova
YOSIYA
ULAMULILO WAKE WONSE
Anafunafuna Yehova
Anayeletsa Yuda ndi Yerusalemu
Anakonza nyumba ya Yehova; anapeza buku la Cilamulo ca Yehova