CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 37–38
Maguwa Ansembe a pa Cihema Komanso Nchito Yawo pa Kulambila Koona
37:25, 29; 38:1
Maguwa ansembe a pa cihema anamangidwa motsatila malangizo amene Yehova anapeleka, ndipo anali na tanthauzo lapadela.
Mofanana na fungo la zofukiza zosakanizidwa mwaluso, mapemphelo opelekedwa na atumiki a Yehova amam’kondweletsa iye
Yehova anali kulandila nsembe zopelekedwa pa guwa lansembe zopseleza. Guwali linali kukhala kutsogolo kwa malo opatulika. Izi zitikumbutsa kuti kukhulupilila nsembe ya dipo la Yesu n’kofunika kwambili kuti tiyanjidwe na Mulungu.—Yoh. 3:16-18; Aheb. 10:5-10
Kodi tingawakonze bwanji mapemphelo athu monga zofukiza pamaso pa Mulungu?—Sal. 141:2