CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | NEHEMIYA 9–11
Olambila Okhulupilika Amacilikiza Dongosolo la Gulu la Mulungu
Anthu a Mulungu anacilikiza kulambila koona ndi mtima wonse m’njila zambili
10:28-30, 32-39; 11:1, 2
Aisiraeli anakonzekela ndi kucita Cikondwelelo ca Misasa m’njila yoyenelela.
Anthu anali kusonkhana tsiku lililonse kuti amvetsele Cilamulo ca Mulungu cikamaŵelengedwa, ndipo anali kusangalala kwambili.
Anthu anali kulapa macimo ao ndi kupemphela kuti Yehova awadalitse.
Anthu anavomeleza kucilikiza dongosolo la gulu la Mulungu.
Kucilikiza dongosolo la gulu la Mulungu kunali kuphatikizapo:
Kumanga banja ndi anthu okhawo amene anali kulambila Yehova
Kupeleka ndalama
Kusunga Sabata
Kupeleka nkhuni ku guwa lansembe
Kupeleka zipatso zoyambilila kuca, ndi mwana woyamba kubadwa wa nyama iliyonse kwa Yehova