CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | ESITERE 6-10
Esitere Anaimila Yehova ndi Anthu Ake
Esitere anali wolimba mtima ndiponso woganizila ena poimila Yehova ndi anthu ake
8:3-5, 9
Esitere ndi Moredekai anali otetezeka. Koma lamulo la Hamani lonena kuti Ayuda onse aphedwe, linali kulengezedwabe m’madela onse a ufumuwo
Kaciŵilinso, Esitere anaika moyo wake paciswe n’kukaonekela pamaso pa mfumu asanaitanidwe. Iye analila ndi kucondelela mfumu kuti isinthe ciwembu cimene Hamani anakonzela Ayuda
Malamulo amene mfumu yakhazikitsa sanali kusinthidwa. Conco, mfumu inapatsa mphamvu Esitere ndi Moredekai yakuti akhazikitse lamulo lina latsopano
Yehova anathandiza kwambili anthu ake kuti apambane
8:10-14, 17
Lamulo latsopano lopatsa Ayuda ufulu wodziteteza linakhazikitsidwa
Anthu okwela pamahachi anatumizidwa m’zigawo zonse za ufumuwo, ndipo Ayuda anayamba kukonzekela nkhondo
Anthu ambili anaona kuti Mulungu anateteza anthu ake, ndipo io analoŵa Ciyuda