CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | SALIMO 1-10
Kuti Tikhale Pamtendele ndi Yehova, Tifunika Kulemekeza Mwana Wake, Yesu
Ulosi unakambilatu kuti anthu adzatsutsa ulamulilo wa Yehova ndi Yesu
2:1-3
Ulosi unakambilatu kuti anthu amitundu adzakana ulamulilo wa Yesu, koma adzafuna kumadzilamulila
Ulosi umenewu unakwanilitsidwa koyamba m’nthawi ya Yesu, ndipo masiku ano ukukwanilitsidwa pamlingo waukulu
Wamasalimo analemba kuti mitundu ya anthu ikung’ung’udza za cinthu copanda pake, kutanthauza kuti zolinga zao n’zopanda pake ndipo zidzalepheleka
Anthu amene amalemekeza Mfumu yodzozedwa ndi Yehova, ndiwo adzalandila moyo
2:8-12
Onse amene amatsutsa Mfumu Mesiya adzaonongedwa
Amene amalemekeza Mwana wa Mulungu, Yesu, ndi amene adzatetezedwa ndi kupeza mtendele