CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 60–68
Tamandani Yehova Womvela Pemphelo
Zimene timalonjeza Yehova, tizizichula m’mapemphelo athu
61:1, 8
Kuchula malonjezo athu m’pemphelo kudzatithandiza kuwasunga
Kudzipeleka kwa Mulungu ndilo lonjezo lofunika kwambili kuposa onse
Hana
Onetsani kuti mumam’dalila Yehova mwa kumukhutulila nkhawa zanu zonse popemphela
62:8
Pemphelo locokela pansi pa mtima n’limene timafotokoza mmene timvelela
Kufotokoza zinthu mosapita mbali m’pemphelo, kudzatithandiza kudziŵa kuti Yehova wayankha pemphelo lathu
Yesu
Yehova amamvela mapemphelo a anthu a maganizo oyenela
65:1, 2
Yehova amamvela mapemphelo a “anthu osiyanasiyana”, amene amafuna kumudziŵa ndi kucita cifunilo cake
Tingapemphele kwa Yehova nthawi iliyonse imene tifuna
Koneliyo
Lembani nkhani zimene mufuna kuchula m’mapemphelo anu: