September 19-25
MASALIMO 135-141
Nyimbo 59 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Tinapangidwa Modabwitsa”: (Mph. 10)
Sal. 139:14—Tikamaganizila za nchito za Yehova, timayamba kumukonda kwambili n’kukhala ndi mtima woyamikila (w07 6/15-CN, tsa. 21 ndime 1-4)
Sal. 139:15, 16—Majini ndi maselo athu amaonetsa mphamvu ndi nzelu za Yehova (w07 6/15-CN, tsa. 22-23 ndime 7-11)
Sal. 139:17, 18—Anthu ndi apadela kwambili cifukwa cakuti ali na nzelu zokwanitsa kukamba ndi kuganiza (w07 6/15-CN, tsa. 23 ndime 12-13; w06 9/1-CN, tsa. 16 ndime 8)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Sal. 136:15—Kodi vesi iyi itithandiza bwanji kumvetsetsa nkhani ya m’buku la Ekisodo? (it-1, tsa. 783 ndime 5)
Sal. 141:5—Kodi Mfumu Davide anazindikila ciani? (w15 4/15, tsa. 31 ndime 1)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Sal.139:1-24
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) wp16. Na. 5 tsa. 16
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) wp16. Na. 5 tsa. 16—Itanilani mwininyumba kumisonkhano.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) fg phunzilo 8, ndime 8—Thandizani wophunzila kuti aziseŵenzetsa mfundo zimene waphunzila.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
“Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo”: (Mph. 15) Mukakambilana nkhani yonse, tambitsani ndi kukambilana vidiyo ya mbali ziŵili, imene ionetsa citsanzo coipa na citsanzo cabwino ca mmene tingaphunzitsile poseŵenzetsa buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse pa tsamba 29, ndime 7. Ngati n’zosatheka kutamba vidiyo, citani zitsanzo ziŵili zosiyana pofuna kumveketsa mfundo zili pa tsamba 8. Ofalitsa afunika kutsatila m’buku lawo. Kumbutsani amene amapatsidwa mbali za ana a sukulu kuti ayenela kupewa zizoloŵezi zimenezi kuti azitsiliza mbali zawo pa nthawi yoyenela.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) kr Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila, ndi nkhani 1, ndime 1-10
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 30 na Pemphelo