LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 October tsa. 5
  • Nzelu ni Zabwino Kwambili Kuposa Golide

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Nzelu ni Zabwino Kwambili Kuposa Golide
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Nzelu Yeniyeni Imafuula
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 October tsa. 5

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MIYAMBO 12–16

Nzelu ni Zabwino Kwambili Kuposa Golide

Yopulinta
Pa sikelo pali mipukutu yolemela kuposa ndalama za golide

N’cifukwa ciani nzelu zocokela kwa Mulungu ni zapamwamba? Zimathandiza munthu kupewa njila zoipa na kusunga moyo wake. Zimamuthandizanso kukhala na maganizo abwino, kukamba zabwino ndi kucita zabwino.

Nzelu zimatithandiza kupewa kunyada

16:18, 19

  • Munthu wodzikuza

    Munthu wanzelu amadziwa kuti Yehova ndiye Gwelo la nzelu zonse

  • Anthu amene acita zinthu zapamwamba kapena amene apatsidwa maudindo, afunika kupewa kunyada ndi kudzikuza

Nzelu zimalimbikitsa munthu kukamba mau abwino

16:21-24

  • Munthu akamba ndipo mnzake amvetsela

    Munthu wanzelu amayesetsa kuona zabwino mwa ena ndi kukamba zabwino zokhudza iwo

  • Mau anzelu amakhala okopa ndi okoma ngati uci, osati aukali kapena a mikangano

KODI MUDZIŴA?

Cisa ca uci

Uci umagaika mosavuta ndipo umabweletsa mphamvu mwamsanga m’thupi. Ni wofunika cifukwa ca kunzuna kwake ndiponso ni mankhwala.

Mau abwino amatsitsimula mwauzimu monga mmene uci ulili wofunika ku thupi la munthu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani