CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MIYAMBO 27–31
Baibo Imakamba za Mkazi Wabwino
Pa Miyambo caputa 31 pali uthenga wofunika umene mayi a Mfumu Lemueli anam’patsa. Malangizo ake anzelu anamuthandiza kudziŵa mmene mkazi wabwino amakhalila.
Mkazi wabwino amakhala wodalilika
31:10-12
Amapeleka malingalilo othandiza pa zosankha za pabanja, koma amakhalabe wogonjela
Mwamuna wake samukaikila kuti adzasankha zocita mwanzelu, ndipo safuna kuti mkaziyo azipempha cilolezo nthawi zonse akafuna kucita zinthu
Amakhala wakhama pa nchito
31:13-27
Sawononga ndalama ndipo amakhala wodzimana n’colinga cakuti banja lake lizivala bwino, kuoneka bwino, ndi kukhala na cakudya cokwanila
Amaseŵenza mwakhama ndi kuyang’anila zocitika za pabanja pake nthawi zonse
Mkazi wabwino amakhala wauzimu
31:30
Amaopa Mulungu ndi kukhala naye pa ubwenzi wolimba