LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 November tsa. 2
  • “Mwamuna Wake Amadziŵika Pazipata”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Mwamuna Wake Amadziŵika Pazipata”
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Baibo Imakamba za Mkazi Wabwino
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • “Mutu wa Mkazi Ndi Mwamuna”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 November tsa. 2

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

“Mwamuna Wake Amadziŵika Pazipata”

Mkazi wabwino amapeleka cithunzi cabwino ca mwamuna wake. M’masiku a Mfumu Lemueli, mwamuna amene anali na mkazi wabwino anali ‘kudziŵika pazipata.’ (Miy. 31:23) Masiku ano, amuna a mbili yabwino amatumikila monga akulu ndi atumiki othandiza. Ngati ni okwatila, utumiki wawo umadalila kwambili pa khalidwe labwino la akazi awo ndi thandizo lawo. (1 Tim. 3:4, 11) Akazi a conco amayamikilidwa kwambili ndi amuna awo ndiponso mpingo.

Mkazi akamba na mwamuna wake mokoma mtima, asamalila ana ake pamene mwamuna wake asamalila nkhani za mumpingo, ndipo mkaziyo agula zakudya

Mkazi wabwino amathandiza mwamuna wake kutumikila mwa. . .

  • kumulimbikitsa na mau abwino.—Miy. 31:26

  • kugaŵana mwamuna wakeyo ndi mpingo.—1 Ates. 2:7, 8

  • kukhala na umoyo wosalila zambili.—1 Tim. 6:8

  • kusamufunsa zinsinsi za mumpingo.—1 Tim. 2:11, 12; 1 Pet. 4:15

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani