LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 November tsa. 3
  • Baibo Imakamba za Mkazi Wabwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Baibo Imakamba za Mkazi Wabwino
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • “Mwamuna Wake Amadziŵika Pazipata”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • “Mutu wa Mkazi Ndi Mwamuna”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 November tsa. 3

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MIYAMBO 27–31

Baibo Imakamba za Mkazi Wabwino

Pa Miyambo caputa 31 pali uthenga wofunika umene mayi a Mfumu Lemueli anam’patsa. Malangizo ake anzelu anamuthandiza kudziŵa mmene mkazi wabwino amakhalila.

Mkazi wabwino amakhala wodalilika

Mkazi wa m’nthawi zakale apeleka cakudya ku banja lake

31:10-12

  • Amapeleka malingalilo othandiza pa zosankha za pabanja, koma amakhalabe wogonjela

  • Mwamuna wake samukaikila kuti adzasankha zocita mwanzelu, ndipo safuna kuti mkaziyo azipempha cilolezo nthawi zonse akafuna kucita zinthu

Amakhala wakhama pa nchito

Mkazi wa m’nthawi zakale apela tiligu

31:13-27

  • Sawononga ndalama ndipo amakhala wodzimana n’colinga cakuti banja lake lizivala bwino, kuoneka bwino, ndi kukhala na cakudya cokwanila

  • Amaseŵenza mwakhama ndi kuyang’anila zocitika za pabanja pake nthawi zonse

Mkazi wabwino amakhala wauzimu

Mkazi apemphela

31:30

  • Amaopa Mulungu ndi kukhala naye pa ubwenzi wolimba

KODI MUDZIŴA?

Miyala ya korali inali yodula kwambili m’nthawi zakale. Inali yokongola, siinali kupezeka-pezeka, ndipo panali kufunika khama kuti munthu aipeze. Miyalayi inali kupezeka m’nyanja ya Mediterranean ndi mu Nyanja Yofiila. Inali malonda ofunika kwambili.

Mwala wa korali

Baibo imaonetsa kuti miyala ya korali ni yamtengo wapatali. Imachula miyalayi mofanana ndi mmene imachulila miyala ina monga golide, siliva, ndi safiro.

Mau a Mulungu amakamba kuti mkazi wabwino ni wamtengo wapatali kuposa “miyala yamtengo wapatali.”—Miy. 31:10.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani