LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 December tsa. 3
  • “Tiyeni Tipite Kukakwela Phili la Yehova”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Tiyeni Tipite Kukakwela Phili la Yehova”
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 December tsa. 3

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 1-5

“Tiyeni Tipite Kukakwela Phili la Yehova”

2:2, 3

“Masiku otsiliza”

Ni nthawi ino imene tikhalamo

“Phili la nyumba ya Yehova”

Kulambila Yehova kokwezeka ndi koyela

“Mitundu yonse idzakhamukila kumeneko”

Amene amalambila m’njila yoyela amasonkhana mu umodzi

“Bwelani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwela phili la Yehova”

Olambila oona amaitana anthu ena kuti azilambila nawo pamodzi

“Iye akatiphunzitsa njila zake, ndipo ife tidzayenda m’njila zakezo.”

Kupitila m’Mau ake, Yehova amatiphunzitsa na kutithandiza kuti tiziyenda m’njila zake

Anthu amitundu yonse akupita ku phili la Yehova

2:4

“Sadzaphunzilanso nkhondo”

Yesaya anafotokoza kuti zida za nkhondo zidzasinthiwa kukhala zolimila, kuonetsa kuti anthu a Yehova adzakhala amtendele. Kodi zida zimenezi zinali ciani m’nthawi ya Yesaya?

‘Malupanga akhala makasu a pulawo’

1 Pulawo inali cida cofala cogawulila nthaka. Mapulawo ena anali ansimbi.—1 Sam. 13:20

‘Mikondo ikhala zida zosadzila mitengo’

2 Cida cosadzila mitengo cinali cimpeni copindika monga comwetela udzu. Cinali codulila mpesa.—Yes. 18:5

Lupanga na mkondo
Pulawo na codulila mitengo
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani