CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 6-10
Ulosi wa Mesiya Umene Unakwanilitsika
Yopulinta
Zaka zambili Yesu akalibe kubadwa, Yesaya analosela kuti Mesiya akayamba kulalikila “m’cigawo ca Yorodano, ku Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.” Yesu anakwanilitsa ulosiwu pamene anali kuyenda m’Galileya monse kulalikila uthenga wabwino.—Yes. 9:1, 2.
Anacita cozizwitsa coyamba—Yoh. 2:1-11 (ku Kana)
Anasankha atumwi ake—Maliko 3:13, 14 (pafupi na Kaperenao)
Analalikila pa phili—Mat. 5:1–7:27 (pafupi na Kaperenao)
Anaukitsa mwana mmodzi yekha wa mayi wamasiye—Luka 7:11-17 (ku Naini)
Anaonekela kwa ophunzila ake 500 pambuyo poukitsidwa—1 Akor. 15:6 (ku Galileya)