Timadziŵa za Mulungu Kucokela kwa Aneneli Ake
Kale-kale, Mulungu anali kuuza anthu ake mauthenga ofunika kupitila mwa aneneli ake. Kodi mauthengawa angatithandize kudziŵa mmene tingalandilile madalitso a Mulungu? Inde angatithandize. Tiyeni tione zimene tingaphunzile kwa aneneli atatu okhulupilika.
ABULAHAMU
Mulungu alibe tsankho ndipo amafuna kudalitsa anthu onse.
Mulungu analonjeza mneneli Abulahamu kuti, “Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso cifukwa ca iwe.”—Genesis 12:3.
Kodi tiphunzilapo ciani? Mulungu amatikonda kwambili ndipo amafuna kudalitsa mabanja onse amene amamumvela, amuna, akazi komanso ana.
MOSE
Mulungu ni wacifundo ndipo amadalitsa anthu amene amayesetsa kum’dziŵa.
Wamphamvuzonse anapatsa mneneli Mose mphamvu yocita zozizwitsa zazikulu. Ngakhale n’conco, Mose anapemphela kuti: “Ndidziwitseni njila zanu, kuti ndikudziweni, kutinso mundikomele mtima [muniyanje].” (Ekisodo 33:13) Mulungu anakondwela na pemphelo la Mose, cakuti anamuthandiza kudziŵa bwino na kumvetsetsa njila zake, komanso makhalidwe ake. Mwacitsanzo, Mose anadziŵa kuti Mlengi ni “Mulungu wacifundo ndi wacisomo.”—Ekisodo 34:6, 7.
Kodi tiphunzilapo ciani? Mulungu amafuna kutidalitsa tonsefe, malinga ngati tiyesetsa kum’dziŵa bwino, kaya ndife amuna, akazi kapena ana. Kupitila m’Malemba Oyela, iye amationetsa mmene tingam’lambilile, komanso kuti ni wofunitsitsa kutiyanja na kutidalitsa.
YESU
Yesu mwacifundo anacilitsa matenda a mtundu uliwonse
Tingapeze madalitso osatha a Mulungu ngati tiphunzila za Yesu na zimene anacita komanso kuphunzitsa.
M’Mawu a Mulungu, timapezamo zambili zokhudza umoyo wa Yesu komanso zimene anaphunzitsa. Mulungu anapatsa Yesu mphamvu yocita zozizwitsa zambili zazikulu, monga kucilitsa akhungu, ogontha, komanso olemala. Iye anaukitsa ngakhale akufa. Conco, Yesu anaonetsa madalitso amene Mulungu adzapeleka kwa anthu kutsogolo. Anafotokoza mmene aliyense wa ife angapezele madalitso amenewa. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.
Yesu anali wacifundo, wacikondi cacikulu, komanso wokoma mtima. Amuna ndi akazi, ana ndi acikulile, onse anapita mwaunyinji kwa iye ataŵapempha mwacikondi kuti: “Phunzilani kwa ine, cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mateyu 11:29) Mosiyana ndi ena a m’nthawi yake amene sanali kulemekeza akazi, Yesu anali kucita zinthu na akazi mokoma mtima komanso moŵalemekeza.
Kodi tiphunzilapo ciani? Yesu anaonetsa cikondi cacikulu kwa anthu, ndipo anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tiyenela kucitila zinthu ndi ena.
YESU SI MULUNGU
Malemba Oyela amaphunzitsa kuti “kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi,” na kuti Yesu Khristu anali mthenga wodzicepetsa wa Mulungu. (1 Akorinto 8:6) Yesu anakamba momveka bwino kuti Mulungu ni wamkulu kwa iye, ndipo Mulungu ndiye anam’tuma kubwela padziko lapansi.—Yohane 11:41, 42; 14:28.a
a Kuti mudziŵe zambili za Yesu Khristu, onani cigawo 8 na 9 m’kabuku kakuti Real Faith—Your Key to a Happy Life kopezeka pa intaneti pa www.jw.org.