CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 58-62
“Ndikalengeze za Caka ca Yehova Cokomela Anthu Mtima”
“Caka ca Yehova cokomela anthu mtima” si caka ceni-ceni
61:1, 2
Ni nthawi imene Yehova amapatsa anthu ofatsa mpata wolabadila ufulu umene iye akulengeza
M’zaka 100 zoyambilila, caka cokomela anthu mtima cinayamba pamene Yesu anayamba utumiki wake mu 29 C.E, ndipo cinatha pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E., “pa tsiku lobwezela” la Yehova.
M’nthawi yathu ino, caka cokomela anthu mtima cinayamba pamene Yesu analongedwa ufumu mu 1914, ndipo cidzatha pa cisautso cacikulu
Yehova adalitsa anthu ake ndi “mitengo ikulu-ikulu ya cilungamo”
61:3, 4
Kaŵili-kaŵili mitengo itali-itali imakulila pamodzi m’nkhalango, ndipo mtengo uliwonse umacilikiza unzake
Mizu ya mitengo imapotana-potana, kumanganitsa mitengoyo pansi, cakuti siingagwe na cimphepo camkuntho
Mitengo itali-italiyo imapeleka mthunzi ku tumitengo tung’ono-tung’ono na zomela zina, ndipo masamba amene amagwa amacititsa nthaka kukhala yaconde
Abale na alongo onse mumpingo wacikhristu padziko lonse, amapindula ndi citetezo na cicilikizo ca “mitengo ikulu-ikulu ya cilungamo,” imene ni otsalila odzozedwa