UMOYO WACIKHRISTU
Muziseŵenzentsa Zofalitsa Zanu Mwanzelu
Yesu anaphunzitsa kuti “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.” (Mat. 10:8) Potsatila malangizo omveka bwino amenewa, sitigulitsa mabaibo kapena zofalitsa zathu. (2 Akor. 2:17) Koma zofalitsa zimenezi zili na coonadi camtengo wapatali ca Mau a Mulungu. Kuti zipulintidwe ndi kutumizidwa ku mipingo padziko lonse, pamacitika nchito yaikulu komanso pamawonongeka ndalama zambili. Conco, tiyenela kutenga mlingo wofunikila cabe.
Tizisamalanso pogaŵila zofalitsa kwa anthu, ngakhale pa ulaliki wapoyela. (Mat. 7:6) M’malo mongogaŵila aliyense amene wapitilapo, yesani kukambako nawo kuti muone ngati ali na cidwi. Kuti mudziŵe, onani ngati mungayankheko kuti ‘inde’ pa iliyonse ya mafunso ali pa danga lili pansili. Ngati simuonapo cidwi kweni-kweni, ni bwino kum’patsa kapepa ka uthenga. Koma ngati wacita kupempha magazini kapena cofalitsa cina, m’patseni mwacimwemwe.—Miy. 3:27, 28