May 29–June 4
YEREMIYA 49-50
Nyimbo 102 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yehova Amadalitsa Odzicepetsa ndi Kulanga Odzitukumula”: (10 min.)
Yer. 50:4-7—Aisiraeli olapa ndi odzicepetsa amene anatsalapo, anali kudzamasulidwa mu ukapolo ndi kubwelela ku Ziyoni
Yer. 50:29-32—Babulo anali kudzawonongedwa cifukwa codzitukumula pamaso pa Yehova (it-1 peji 54)
Yer. 50:38, 39—Anati ku Babulo sikudzakhalanso anthu (jr peji 161 pala. 15; w98 4/1 peji 20 pala. 20)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yer. 49:1, 2—N’cifukwa ciani Aamoni anadzudzulidwa ndi Yehova? (it-1 peji 94 pala. 6)
Yer. 49:17, 18—Kodi Edomu anakhala bwanji monga Sodomu na Gomora? Ndipo n’cifukwa ciani? (jr peji 163 pala. 18; ip-2 peji 351 pala. 6)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yer. 50:1-10
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) T-32—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) T-32—Kambilanani mbali yakuti “Ganizilani Funso Ili.” Yalani maziko a ulendo wotsatila.
Nkhani: (6 mineti kapena kucepelapo) w15 3/15 peji 17—Mutu Wake: M’zaka Zapitazi, N’cifukwa Ninji Mabuku Athu Sakambapo Kaŵili-kaŵili za Zinthu Zocitila Mthunzi ndi Zocitilidwa Mthunzi?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Cotsani Mtanda wa Denga: (15 min.) Tambitsani vidiyo yakuti Cotsani Mtanda wa Denga (yendani ku mavidiyo BAIBULO). Ndiyeno kambilanani mafunso aya: Kodi m’bale anaonetsa bwanji mzimu wonyada ndi wosuliza? Cinam’thandiza n’ciani kusintha kaganizidwe kake? Nanga anapindula bwanji?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 13 mapa. 11-23
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 131 na Pemphelo