CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YEREMIYA 49-50
Yehova Amadalitsa Odzicepetsa ndi Kulanga Odzitukumula
50:4-7
Aisiraeli olapa anagwetsa misozi ya cisangalalo pamene Yehova anawamasula mu ukapolo
Anakumbukilanso pangano lawo ndi iye na kuyenda ulendo wautali wobwelela ku Yerusalemu kukabwezeletsa kulambila koona
50:29, 39
Ababulo odzikuzawo sanapulumuke cilango pocita nkhanza zaunkhalwe kwa anthu a Yehova
Monga mwa ulosi, Babulo anasanduka matongwe osakhalamo anthu