CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YEREMIYA 39-43
Yehova Adzaweluza Aliyense Malinga na Nchito Zake
Zedekiya sanamvele malangizo a Yehova akuti adzipeleke okha kwa a Babulo
39:4-7
Ana a Zedekiya anaphedwa iye akuona. Ndiyeno iye anabowoledwa maso, kumangidwa m’matangadza a unyolo, ndi kuponyedwa m’ndende ku Babulo mpaka imfa yake
Ebedi-meleki anakhulupilila mwa Yehova ndi kudela nkhawa Yeremiya mneneli wa Mulungu
39:15-18
Yehova analonjeza kuti adzateteza Ebedi-meleki pa kuwonongedwa kwa Isiraeli
Yeremiya analalikila molimba mtima kwa zaka zambili Yerusalemu asanawonongedwe
40:1-6
Yehova anateteza Yeremiya pamene Yerusalemu anazingidwa, ndipo analinganiza kuti Ababulo am’masule