CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EZEKIELI 1-5
Ezekieli Anasangalala Polengeza Uthenga wa Mulungu
M’masomphenya, Yehova anapatsa Ezekieli mpukutu na kumuuza kuti adye mpukutuwo. Kodi zimenezi zinatanthauza ciani?
2:9–3:2
Ezekieli anafunika kuumvetsetsa uthenga wa Mulungu. Kusinkha-sinkha pa mau a mpukutuwo kunam’fika pamtima Ezekieli ndi kum’sonkhezela kulankhula
3:3
Mpukutuwo unali wonzuna cifukwa Ezekieli anali kuona utumiki wake moyenela