UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muzisangalala Polalikila Uthenga Wabwino
Kodi zinakuvutamponi kulalikila? Ambili a ife tingayankhe kuti inde. Cifukwa ciani? Mwina nthawi zambili timapeza anthu alibe cidwi ndi okwiya m’gawo lathu kapena timaopa kukamba ndi anthu amene sitidziŵa. Kukamba zoona, izi zingatilande cimwemwe. Komabe, timalambila Mulungu wacimwemwe amene amafuna kuti tizim’tumikila mwacimwemwe. (Sal. 100:2; 1 Tim. 1:11) Ni zifukwa zitatu ziti zimene tiyenela kukhalila osangalala polalikila?
Coyamba, timalalikila uthenga wopatsa ciyembekezo. Olo kuti anthu m’dzikoli alibe ciyembekezo, tingatsitsimule mitima yawo ndi “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yes. 52:7) Ndipo uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umatipatsa cimwemwe. Musanapite kukalalikila, sinkha-sinkhani pa madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweletsa padziko lapansi.
Caciŵili, uthenga wabwino umene timalalikila umapindulitsa anthu kuthupi na kuuzimu. Amaphunzila kuleka kucita zoipa na kukhala na ciyembekezo ca moyo wamuyaya. (Yes. 48:17, 18; Aroma 1:16) Tizikumbukila kuti nchito yathu ili monga yopulumutsa anthu pakagwa tsoka. Ngakhale kuti ena safuna kupulumutsidwa, timapitiliza kusakila amene afuna.—Mat. 10:11-14.
Cacitatu ndiponso cofunika kwambili n’cakuti ulaliki wathu umalemekeza Yehova. Iye amaona nchitoyi kukhala yofunika ngako. (Yes. 43:10; Aheb. 6:10) Kuwonjezela apo, amatipatsa mzimu woyela mowolowa manja kuti tikwanilitse nchitoyi. Conco, condelelani Yehova kuti akupatseni cimwemwe, cimene ni khalidwe limene mzimu woyela umatulutsa. (Agal. 5:22) Ndi thandizo lake, tingathetse nkhawa na kuyamba kulalikila molimba mtima. (Mac. 4:31) Zikakhala conco, olo kuti tikumane na anthu abwanji m’gawo, tidzakhala na cimwemwe m’nchito yolalikila.—Ezek. 3:3.
Kodi mungakonde kuonetsa khalidwe lanji mu utumiki? Kodi mungaonetse bwanji cimwemwe?
TAMBANI VIDIYO YAKUTI PEZANINSO CIMWEMWE MWA KUPHUNZILA NA KUSINKHA-SINKHA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
N’cifukwa ciani kuphunzila Baibo n’kofunika maningi, olo kuti timathela maola ambili kulalikila mwezi uliwonse?
Kodi tingatengele Mary m’njila yanji?
Kodi mumasinkha-sinkha Mau a Mulungu panthawi iti?
N’ciani cimakupatsani cimwemwe polalikila uthenga wabwino?