June 26–July 2
EZEKIELI 6-10
Nyimbo 141 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kodi Mudzaikidwa Cizindikilo Kuti Mudzapulumuke?”: (10 min.)
Ezek. 9:1, 2—Masomphenya a Ezekieli akutiphunzitsa mfundo zothandiza (w16.06 peji 31-32)
Ezek. 9:3, 4—Amene amalandila uthenga umene timalalikila adzaikiwa cizindikilo kuti adzapulumuke mkati mwa cisautso cacikulu
Ezek. 9:5-7—Yehova sadzaononga anthu olungama pamodzi na oipa
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Ezek. 7:19—Kodi vesili likutithandiza bwanji kukonzekela zamtsogolo? (w09 9/15 peji 23 pala. 10)
Ezek. 8:12—Kodi vesili lionetsa bwanji kuti kusoŵa cikhulupililo kungacititse munthu kucita chimo? (w11 4/15 peji 26 pala. 14
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Ezek. 8:1-12
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) Chiv. 4:11—Phunzitsani Coonadi.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) Sal. 11:5; 2 Akor. 7:1—Phunzitsani Coonadi.
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) bh 127 mapa. 4-5—Onetsani mmene mungam’fikile pamtima wophunzila.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Muzitsatila Miyezo ya Yehova ya Makhalidwe Abwino”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Mwamuna M’modzi, Mkazi M’modzi
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 14 mapa. 8-14, na bokosi “Anafa Cifukwa Copeleka Ulemelelo kwa Mulungu”
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 33 na Pemphelo