CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EZEKIELI 6-10
Kodi Mudzaikidwa Cizindikilo Kuti Mudzapulumuke?
Masomphenya a Ezekieli anakwanilitsika koyamba pakuonongedwa kwa Yerusalemu. Nanga masiku ano akukwanilitsika bwanji?
9:1, 2
Munthu amene ananyamula kacikwama ka mlembi aimila Yesu Khristu
Amuna 6 amene ananyamula zida zoonongela aimila asilikali a kumwamba, ndipo Khristu ndiye mtsogoleli wawo
9:3-7
Akhamu lalikulu adzaikiwa cizindikilo pamene adzaweluzidwa kuti ni nkhosa mkati mwa cisautso cacikulu