UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muzitsatila Miyezo ya Yehova ya Makhalidwe Abwino
Yehova Mulungu Anaika miyezo ya makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, anaika lamulo lakuti cikwati ni m’gwilizano wokhalitsa wa pakati pa mwamuna na mkazi. (Mat. 19:4-6, 9) Iye amadana na ciwelewele ca mtundu uliwonse. (1 Akor. 6:9, 10) Anaika mfundo zokhudza mavalidwe na kudzikonza zimene zimasiyanitsa anthu ake.—Deut. 22:5; 1 Tim. 2:9, 10.
Masiku ano, anthu ambili amakana kutsatila miyezo ya Yehova. (Aroma 1:18-32) Iwo amayendela maganizo a anthu pa nkhani ya mavalidwe, kudzikonza na makhalidwe. Ambili amanyadila makhalidwe awo oipa, ndipo amasuliza anthu amene amayendela mfundo zosiyanako na zawo.—1 Pet. 4:3, 4.
Monga Mboni za Yehova, tifunika kutsatila mfundo za makhalidwe abwino a Mulungu molimba mtima. (Aroma 12:9) Motani? Tiyenela kuuza ena mwanzelu cimene cili covomelezeka kwa iye. Kuonjezela apo, tiyenela kutsatilabe miyezo yake ya makhalidwe abwino mu umoyo wathu. Mwacitsanzo, posankha zovala ndi kudzikonza tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi zosankha zanga zimaonetsa kuti nimatsatila miyezo ya Yehova kapena ya dziko?’ Nanga mavalidwe na kudzikonza kwanga zimaonetsa kuti ndine Mkhristu woopa Mulungu? Posankha pulogilamu ina yake kapena filimu yotamba, tingadzifunse kuti: ‘Kodi Yehova amavomeleza pulogilamuyi? Nanga ilimbikitsa mfundo za makhalidwe andani? Kodi zosangulutsa zimene nimakonda zinganisonkhezele kucita zoipa? (Sal. 101:3) Kodi zingakhumudwitse a m’banja langa ndi anzanga?’—1 Akor. 10:31-33.
N’cifukwa ciani mpofunika kwambili kuti tizitsatila miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino? Posacedwapa Khristu Yesu adzawononga mitundu ya anthu na kuipa konse. (Ezek. 9:4-7) Amene akucita cifunilo ca Mulungu ni okhawo amene adzakhalapo. (1 Yoh. 2:15-17) Conco, tiyeni tipitilize kutsatila miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino kuti anthu amene akucitila umboni za makhalidwe athu abwino atamande Mulungu.—1 Pet. 2:11, 12.
Kodi mavalidwe na kudzikonza kwanga zimaonetsa kuti nimayendela miyezo yabwanji?
TAMBANI VIDIYO YAKUTI KHALA BWENZI LA YEHOVA—MWAMUNA M’MODZI, MKAZI M’MODZI, NDIYENO KAMBILANANI MAFUNSO AYA:
N’cifukwa ciani n’cinthu ca nzelu kutsatila miyezo ya Yehova?
N’cifukwa ciani makolo ayenela kuyamba kuphunzitsa ana awo mfundo za makhalidwe abwino akali aang’ono?
Kodi acicepele ndi acikulile omwe angathandize bwanji anthu kupindula na ubwino wa Mulungu?