Cimwemwe Khalidwe Locokela kwa Mulungu
MUNTHU aliyense amafuna kukhala na umoyo wacimwemwe. Koma m’masiku ano otsiliza, tonse timakumana na mayeselo ovuta kuwapilila. (2 Tim. 3:1) Kupanda cilungamo, matenda, ulova, imfa, ndi mavuto ena, pang’ono m’pang’ono zingacititse ena kukhala opanda cimwemwe. Ngakhale atumiki a Mulungu angafooke ndipo cimwemwe cawo cingathe. Ngati izi zakucitikilani, kodi mungacite ciani kuti mukhalenso na cimwemwe?
Kuti tipeze yankho pa funso limeneli, coyamba tifunika kumvetsetsa tanthauzo la cimwemwe ceni-ceni, ndi mmene ena akhalilabe acimwemwe olo kuti amakumana na mavuto. Ndiyeno, tidzakambilana zimene tingacite kuti tikhalebe na cimwemwe ndi mmene tingacikulitsile.
KODI CIMWEMWE N’CIANI?
Kukhala wacimwemwe sikutanthauza kukhala wansangala cabe kapena woseka-seka. Tiyelekezele motele: Pambuyo pakuti cakolwa wamwa moŵa kwambili, angakhale woseka-seka. Koma akayanganuka kapena kuti kukololoka, sakhalanso woseka-seka ndipo amabwelelanso ku umoyo wake wodzala na mavuto na cisoni. Cisangalalo cake cakanthawi si cimwemwe ceni-ceni.—Miy. 14:13.
Mosiyana ndi zimenezi, cimwemwe ni khalidwe lokhazikika la mu mtima. Cimwemwe cimatanthauza, “kumva bwino mu mtima cifukwa copeza kapena kuyembekezela zabwino.” Munthu wacimwemwe amakhalabe wokondwa mosasamala kanthu kuti ali pa mtendele kapena ayi. (1 Ates. 1:6) Ndi iko komwe, munthu angakumane na vuto linalake, koma n’kukhalabe na cimwemwe mu mtima. Mwacitsanzo, atumwi anakwapulidwa cifukwa colalikila za Khristu. Komabe, iwo “anacoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala cifukwa cakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucitilidwa cipongwe cifukwa ca dzina la Yesu.” (Mac. 5:41) Mwacionekele, atumwiwo sanali kusangalala cifukwa cokwapulidwa. Koma monga atumiki a Mulungu, anapeza cimwemwe ceni-ceni cifukwa cokhala okhulupilika kwathunthu kwa iye.
Cimwemwe cotelo siticita kubadwa naco ndiponso sicibwela cokha. Cifukwa ciani zili conco? Cifukwa cakuti cimwemwe ceni-ceni ni mbali ya cipatso ca mzimu woyela wa Mulungu. Mwa thandizo la mzimu wa Mulungu, tingavale mokwanila “umunthu watsopano,” umene umaphatikizapo khalidwe la cimwemwe. (Aef. 4:24; Agal. 5:22) Ndipo kukhala acimwemwe kumatithandiza kupilila mavuto amene timakumana nawo mu umoyo.
ZITSANZO ZIMENE TIFUNIKA KUTENGELA
Yehova anali kufuna kuti pa dziko lapansi pazicitika zinthu zabwino, osati zoipa zimene timaona kaŵili-kaŵili masiku ano. Komabe, zoipa zimene anthu amacita sizim’landa cimwemwe. Mau a Mulungu amati: “Pokhala pake pali mphamvu ndi cimwemwe.” (1 Mbiri 16:27) Kuwonjezela apo, zinthu zabwino zimene atumiki ake amacita ‘zimakondweletsa mtima wake.’—Miy. 27:11.
Tingatengele citsanzo ca Yehova mwa kupewa kuda nkhawa kwambili ngati zinthu sizinayende mmene tinali kuyembekezela. Kuti tisataye cimwemwe cathu, tiyenela kuika maganizo athu pa zabwino zimene tili nazo pa nthawi ino, na kuyembekezela moleza mtima madalitso am’tsogolo.a
M’Baibo mulinso zitsanzo za anthu amene anakhalabe acimwemwe olo kuti anakumana na mavuto. Abulahamu ni mmodzi mwa iwo. Iye anapilila mavuto aakulu oika moyo wake paciopsezo na zoipa zina zimene anthu ena anam’citila. (Gen. 12:10-20; 14:8-16; 16:4, 5; 20:1-18; 21:8, 9) Ngakhale zinali conco, Abulahamu anakhalabe na cimwemwe mumtima mwake. Cinam’thandiza n’ciani? Anali kuganizila kwambili za ciyembekezo cake cokakhala m’dziko latsopano lolamulidwa na Mesiya. (Gen. 22:15-18; Aheb. 11:10) Yesu anati: “Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezela kuona tsiku langa.” (Yoh. 8:56) Tingatengele citsanzo ca Abulahamu mwa kuganizila zinthu zabwino zimene tidzasangalala nazo m’tsogolo.—Aroma 8:21.
Mofanana ndi Abulahamu, mtumwi Paulo na mnzake Sila nawonso anali kuganizila kwambili za malonjezo a Mulungu. Iwo anali na cikhulupililo colimba, ndipo anakhalabe acimwemwe ngakhale kuti anakumana na mavuto. Mwacitsanzo, atakwapulidwa koopsa na kuponyewa m’ndende, “capakati pa usiku, [iwo]” anayamba “kupemphela ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo.” (Mac. 16:23-25) Paulo na Sila anapeza mphamvu mwa kuganizila za ciyembekezo cawo. Kuwonjezela apo, anakhalabe acimwemwe podziŵa kuti anali kuvutika kaamba ka dzina la Khristu. Na ise tingatengele Paulo na Sila mwa kuganizila zotulukapo zabwino zimene zimakhalapo cifukwa cotumikila Mulungu mokhulupilika.—Afil. 1:12-14.
Masiku ano, m’gulu lathu muli zitsanzo zolimbikitsa za abale na alongo amene anakhalabe na cimwemwe pamene anakumana ndi mavuto. Mwacitsanzo, mu November 2013, cimphepo camphamvu camkuntho cochedwa Haiyan, cinasakaza cigawo capakati ca dziko la Philippines. Cimphepoco cinawononga nyumba za mabanja opitilila 1,000 a Mboni. George, amene nyumba yake inawonongekelatu mumzinda wa Tacloban, anati: “Mosasamala kanthu na zimene zinacitika, abale ni osangalala. Siningakwanitse kufotokoza cimwemwe cimene tili naco.” Tikakumana ndi mavuto aakulu, tidzakhalabe na cimwemwe ngati tiganizila zimene Yehova waticitila komanso kumuyamikila. Kodi Yehova waticitila zinthu zina ziti zimene zingatithandize kukhala na cimwemwe?
ZIFUKWA ZIMENE TIYENELA KUKHALILA ACIMWEMWE
Palibe cina cimene cingatipatse cimwemwe coculuka kuposa kukhala pa ubwenzi na Mulungu. Tangoganizilani: Tili na mwayi wodziŵa Mfumu ya Cilengedwe Conse. Iye ni Atate wathu, Mulungu wathu, ndi Bwenzi lathu!—Sal. 71:17, 18.
Komanso, timayamikila kuti Mulungu anatipatsa moyo, umene timatha kusangalala nawo. (Mlal. 3:12, 13) Popeza tinakokedwa na Yehova, timadziŵa colinga cimene ali naco pa ise. (Akol. 1:9, 10) Pa cifukwa cimeneci, tili na umoyo waphindu ndiponso wokhala na colinga. Koma anthu ambili sadziŵa colinga ca moyo. Pofotokoza kusiyana kumeneku, Paulo analemba kuti: “‘Palibe munthu amene anaonapo kapena kumvapo kapenanso kuganizapo zimene Mulungu wakonzela omukonda.’ Pakuti mwa mzimu wake, Mulungu anaululila ifeyo zinthu zimenezi.” (1 Akor. 2:9, 10) Ndithudi! kudziŵa colinga ca Yehova na cifunilo cake kumatithandiza kukhala acimwemwe.
Onani zinanso zimene Yehova wacitila anthu ake. Iye amatikhululukila macimo athu, ndipo izi zimatithandiza kukhala osangalala. (1 Yoh. 2:12) Komanso, kaamba ka cifundo cake, tili na ciyembekezo codalilika cakuti posacedwa tidzaloŵa m’dziko latsopano. (Aroma 12:12) Cinanso, masiku ano Yehova watipatsa gulu labwino la olambila anzathu. (Sal. 133:1) Kuwonjezela apo, Mau a Mulungu amakamba kuti Yehova amateteza anthu ake kwa Satana na ziŵanda zake. (Sal. 91:11) Tikamaganizila madalitso amenewa ocokela kwa Mulungu, cimwemwe cathu cidzakula.—Afil. 4:4.
MMENE MUNGAKULITSILE CIMWEMWE CANU
Kodi Mkhristu amene ali kale na cimwemwe angathe kucikulitsa? Yesu anati: “Ndalankhula zinthu izi kwa inu, kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, ndi kuti cimwemwe canu cisefukile.” (Yoh. 15:11) Mfundo imeneyi ionetsa kuti n’zotheka kukulitsa cimwemwe cathu. Kukulitsa cimwemwe tingakuyelekezele na kusonkhela moto. Timafunika kusonkhela nkhuni pa moto kuti uyake kwambili. Mofananamo, mufunika kuyesetsa kukhala munthu wauzimu kuti mukulitse cimwemwe canu. Kumbukilani kuti mzimu wa Mulungu ndiwo umakolezela cimwemwe. Conco, mungathe kukhala na cimwemwe coculuka ngati nthawi zonse mumapempha thandizo la mzimu wa Yehova na kusinkha-sinkha Mau ake ouzilidwa na mzimu.—Sal. 1:1, 2; Luka 11:13.
Mungakulitsenso cimwemwe canu mwa kukhala akhama pa nchito zokondweletsa Yehova. (Sal. 35:27; 112:1) N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa tinalengedwa kuti ‘tiziopa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake cifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenela kucita.’ (Mlal. 12:13) M’mau ena, tingakambe kuti tinalengedwa n’colinga cakuti tizicita cifunilo ca Mulungu. Conco, tikamatumikila Yehova, timakhala na umoyo wacimwemwe kwambili.b
MAPINDU AMENE TIMAPEZA CIFUKWA COKHALA ACIMWEMWE
Pamene tikulitsa cimwemwe caumulungu, timapeza mapindu ambili. Mwacitsanzo, timakondweletsa kwambili Atate wathu wakumwamba ngati tim’tumikila mwacimwemwe mosasamala kanthu za mavuto amene takumana nawo. (Deut. 16:15; 1 Ates. 5:16-18) Komanso, tikakhala na cimwemwe ceni-ceni, timapewa umoyo wokonda zinthu zakuthupi. M’malomwake, timayesetsa kukhala odzipeleka kaamba ka Ufumu wa Mulungu. (Mat. 13:44) Tikaona zotulukapo zabwino za kudzipeleka kwathu, cimwemwe cathu cimawonjezeleka, timakhala na umoyo wokhutila, ndiponso timathandiza ena kukulitsa cimwemwe cawo.—Mac. 20:35; Afil. 1:3-5.
“Kaŵili-kaŵili ngati munthu ni wosangalala ndiponso wokhutila mu umoyo wake, amadzakhala na thanzi labwino m’tsogolo.” Izi n’zimene katswili wina wa pa Univesiti ya Nebraska ku United States analemba pambuyo popenda zotsatila za kafukufuku wina wa za umoyo. Mfundo imeneyi ni yogwilizana na zimene Baibo imakamba. Imati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa.” (Miy. 17:22) Ndithudi, ngati mukulitsa cimwemwe canu, mungathe kukhala na thanzi labwino.
Conco, olo kuti tili m’nthawi zovuta, tingathe kukhala na cimwemwe ceni-ceni ndi cokhalitsa. Izi zingatheke mwa mphamvu ya mzimu woyela, umene timaupeza mwa kupemphela, kuphunzila Mau a Yehova na kuwasinkha-sinkha. Timakulitsanso cimwemwe cathu mwa kuganizila madalitso amene tili nawo, kutengela cikhulupililo ca ena, na kuyesetsa kucita cifunilo ca Mulungu. Tikamacita zimenezi, mau a pa Salimo 64:10 adzakwanilitsika mu umoyo wathu. Lembali limati: “Wolungama adzakondwela mwa Yehova ndipo adzathaŵila kwa iye.”
a Khalidwe la kuleza mtima tidzalikambilana m’tsogolo, m’nkhani ina yofotokoza “cipatso ca mzimu.”
b Malangizo ena amene angakuthandizeni kukulitsa cimwemwe canu ali pa kabokosi kakuti, “Zina Zimene Mungacite Kuti Mukulitse Cimwemwe.”