NKHANI YOPHUNZILA 40
NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe
Yehova ndi Amene ‘Amatisangalatsa Kwambili’
“ Ndidzapita . . . kwa Mulungu amene amandisangalatsa kwambili.”—SAL. 43:4.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
M’nkhani ino, tione zinthu zimene zingatilande cimwemwe komanso zimene zingatithandize kuti tikhalenso ndi cimwemwe.
1-2. (a) N’ciani cimacitika pa umoyo wa anthu ambili masiku ano? (b) Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?
ANTHU ambili amacita zilizonse zimene angathe kuti apeze cimwemwe. Ngakhale n’telo, cimwemwe ceniceni sacipeza. M’malomwake, amakhala othedwa nzelu cifukwa cogwilitsidwa mwala ndipo sakhala acimwemwe. Ngakhale anthu a Yehova amamva conco nthawi zina. Popeza tikukhala ‘m’masiku otsiliza,’ tingakumane ndi mabvuto amene angaticititse kukhala acisoni kwambili komanso ankhawa.—2 Tim. 3:1.
2 M’nkhani ino, tikambilana zinthu zimene zingatilande cimwemwe komanso zimene zingatithandize kukhalanso acimwemwe. Koma coyamba, tiyeni tidziwe Gwelo la cimwemwe ceniceni.
GWELO LA CIMWEMWE CENICENI
3. Kodi cilengedwe cimatiphunzitsa ciani ponena za Yehova? (Onaninso zithunzi.)
3 Yehova wakhala wacimwemwe nthawi zonse. Ndipo amafuna kuti nafenso tizikhala osangalala. Umboni wa mfundoyi umaonekela m’zinthu zimene analenga. Timasangalala tikaona dzikoli lomwe muli zinthu za maonekedwe osiyana-siyana, tikaona nyama zikusewela komanso tikamadya cakudya cokoma. Kunena zoona, Mulungu amatikonda kwambili ndipo amafuna kuti tizisangalala nao moyo!
Baby elephant: Image © Romi Gamit/Shutterstock; penguin chicks: Vladimir Seliverstov/500px via Getty Images; baby goats: Rita Kochmarjova/stock.adobe.com; two dolphins: georgeclerk/E+ via Getty Images
Tikaona nyama zikusewela timamvetsa kuti Yehova ndi wacimwemwe (Onani ndime 3)
4. (a) Kodi zimatheka bwanji Yehova kukhalabe wacimwemwe ngakhale kuti amaona mabvuto amene ali padzikoli? (b) Kodi Yehova watipatsa mphatso yanji? (Salimo 16:11)
4 Ngakhale kuti Yehova amaona mabvuto amene anthu akukumana nawo ndipo zimam’khudza kwambili, Baibo imati ndi “Mulungu wa cimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Cifukwa n’cakuti iye adziwa kuti mabvuto onse ndi akanthawi. Ndipo iyemwini ndiye wakonza tsiku limene adzathetseletu cisoni komanso mabvuto onse. Koma palipano, iye akupilila moleza mtima kufikila tsiku pamene adzathetse mabvutowo. Ngakhale n’conco, iye amamvetsa zimene tikukumana nazo ndipo amatithandiza. Kodi amatithandiza motani? Iye amatipatsa mphatso. Mphatsoyi ndi cimwemwe. (Welengani Salimo 16:11.) Tsopano tiyeni tione zimene zinapangitsa Yesu kukhala wacimwemwe.
5-6. N’cifukwa ciani Yesu ndi wacimwemwe?
5 Yesu ndiye wacimwemwe kwambili pa zolengedwa zonse za Yehova. N’cifukwa ciani zili conco? Nazi zifukwa zina. Coyamba, “iye ndiye cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo.” Izi zitanthauza kuti anatengela atate ake ndendende. (Akol. 1:15; 1 Tim. 6:15.) Cinanso, Yesu ndiye wakhala nthawi yaitali kwambili ndi Atate ake amene ndi Gwelo la cimwemwe.
6 Kuonjezela pamenepo, Yesu wakhala akupeza cimwemwe mwa kucita cifunilo ca atate ake. (Miy. 8:30, 31; Yoh. 8:29) Cifukwa ca kukhulupilika kwake, Yehova amasangalala naye kwambili. Ici n’cifukwa cinanso cimene cimapangitsa Yesu kukhala wacimwemwe.—Mat. 3:17.
7. Kodi tingacipeze bwanji cimwemwe ceniceni?
7 Nafenso tingapeze cimwemwe ceniceni tikapitiliza kum’dziwa bwino Yehova, Gwelo la cimwemwe. Tikamathela nthawi yoculuka tikuphunzila za Yehova ndi kutengela citsanzo cake, cimwemwe cathu cimaonjezeka. Timapezanso cimwemwe tikamacita cifunilo ca Mulungu, komanso tikadziwa kuti amasangalala nafe.a (Sal. 33:12) Koma nthawi zina tingakhale opanda cimwemwe kwa kanthawi kapena kwa nthawi yaitali. Kodi zikakhala telo ndiye kuti Mulungu sakusangalala nafe? Kutalitali! Yehova amamvetsa kuti popeza ndife anthu opanda ungwilo, nthawi zina timawawidwa mtima, timakhumudwa, ndi kupsyinjika maganizo. (Sal. 103:14) Tiyeni tikambilane zinthu zimene zingatilande cimwemwe komanso zimene tingacite kuti tikhalenso acimwemwe.
ZINTHU ZIMENE ZINGATILANDE CIMWEMWE
8. Kodi mabvuto angatipangitse kumva bwanji?
8 Coyamba: Mabvuto. Kodi mukubvutika cifukwa ca mazunzo, masoka acilengedwe, umphawi, matenda, kapena ukalamba? Mabvuto ngati amenewa angatilande cimwemwe mosabvuta, maka-maka ngati palibe cimene tingacitepo kapena ngati sitingawathetse. Baibo imanena momveka bwino kuti “munthu sasangalala ngati mtima ukum’pweteka.” (Miy. 15:13) Babis, mkulu amene m’zaka zinai cabe anafeledwa m’bale wake ndi makolo ake onse, anakamba kuti: “N’namva kuti ndili ndekha-ndekha ndipo ndinaona kuti palibe wondithandiza. Makolo anga ndi m’bale wanga asanamwalile, nthawi zina n’nali kubvutika maganizo cifukwa n’nali kufuna kukhala ndi nthawi yokwanila yoceza nao koma sizinali kutheka cifukwa n’nali kukhala wopanikizika ndi zina.” Kunena zoona, mabvuto angatilefule.
9. N’ciani cingatithandize kukhalanso acimwemwe? (Yeremiya 29:4-7, 10)
9 Kodi tingatani kuti tikhalenso acimwemwe? Tingapezenso cimwemwe tikakhala okhutila ndi kubvomeleza mmene zinthu zilili pa umoyo wathu. Dzikoli limalimbikitsa mfundo yakuti tingakhale acimwemwe kokha ngati umoyo wathu ukuyenda mwa myaa! Koma izi si zoona. Mwacitsanzo, Yehova analangiza Ayuda amene anatengedwela ku ukapolo ku Babulo kuti abvomeleze umoyo wao watsopano ndi kuti acite zonse zimene angathe kuti akhale ndi umoyo wacimwemwe ku Babuloko. (Welengani Yeremiya 29:4-7, 10.) Kodi mungaphunzilepo ciani? Muyenela kubvomeleza mmene zinthu zilili pa umoyo wanu panopa, ndipo muziyamikila zabwino zimene muli nazo. Musaiwale kuti Yehova adzakuthandizani. (Sal. 63:7; 146:5) Mlongo wina dzina lake Effie, amene analemala atapezeka mungozi anakamba kuti: “N’nalandila thandizo lalikulu locokela kwa Yehova, kubanja langa, komanso kumpingo. Cotelo, n’naona kuti ngati ndingakhalebe wopanda cimwemwe, zingaonetse kusayamikila. Ndifuna kuonetsa kuti ndimayamikila thandizo lao lalikulu.”
10. Zingatheke bwanji kukhala acimwemwe ngakhale pamene takumana ndi mabvuto?
10 N’zotheka ife ndi a m’banja lathu kukhalabe acimwemwe ngakhale pamene takumana ndi mabvuto aakulu kapena pamene zinthu zoipa kwambili zaticitikila.b (Sal. 126:5) Zingatheke cifukwa cimwemwe cathu sicidalila mmene zinthu zilili pa umoyo. Maria, yemwe ndi mpainiya, ananena kuti: “Kukhalabe wacimwemwe pamene ukukumana ndi mabvuto sikutanthauza kuti ukubisa mmene ukumvela. Koma kumatanthauza kuti sunaiwale malonjezo a Yehova. Atate wathu wakumwamba adzatithandiza kukhalabe acimwemwe.” Musaiwale kuti ngakhale mabvuto athu atakhala aakulu motani, ali ngati mame. Posacedwapa, adzathetsedwa ndipo sadzakumbukilidwanso.
11. Kodi citsanzo ca mtumwi Paulo cingakulimbikitseni bwanji?
11 Koma bwanji mukamaona ngati mabvuto amene mukukumana nao ndi umboni wakuti Yehova sakukondwela nanu? Ngati umu ndi mmene mumaonela, kuganizila za atumiki okhulupilika a Yehova amene anakumanapo ndi mabvuto aakulu kungakuthandizeni. Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Yesu ndi amene anam’sankha kuti akalengeze uthenga wabwino “kwa anthu a mitundu ina komanso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.” (Mac. 9:15) Uwu unali utumiki wapadela! Ngakhale n’telo, Paulo anakumana ndi mabvuto ambili. (2 Akor. 11:23-27) Kodi mabvuto a Paulo ooneka ngati osathelapo unali umboni wakuti Yehova waleka kukondwela naye? Kutalitali! Tikutelo cifukwa kuti Paulo akwanitse kupilila, ndi Yehova anali kum’thandiza. (Aroma 5:3-5) Ndiye tsopano ganizilani mmene zinthu zilili kwa inu. Ngakhale kuti mukukumana ndi mabvuto, mukupilila mokhulupilika. Conco, khalani otsimikiza kuti Yehova akukondwela nanu.
12. Kodi n’ciani cingacitike ngati sitinakwanilitse zolinga zathu potumikila Yehova?
12 Caciwili: Ngati zinthu zimene munali kuyembekezela sizinacitike. (Miy. 13:12) Pofuna kuonetsa kuti timam’konda Yehova ndi kumuyamikila, timadziikila zolinga zauzimu. Komabe ngati zolinga zimene tadziikila sitingazikwanilitse cifukwa ca zobvuta zina, tingafooke. (Miy. 17:22) Mpainiya wina, dzina lake Holly, anati: “N’nali kufuna kukalowako Sukulu ya Alengezi, kukatumikila ku dziko lina, kapena kukagwilako nchito yomanga ku Ramapo. Koma zinthu zinasintha ndipo sindikanakwanilitsa zolinga zimene n’nadziikila. N’nakhumudwa kwambili.” Atumiki ambili a Yehova zaconco zinawacitikilapo.
13. Kodi n’zolinga zina ziti zimene tingadziikile ngati sitingakwanitse kucita zambili cifukwa ca zobvuta zina?
13 Kodi tingatani kuti tikhalenso acimwemwe? Muzikumbukila kuti Yehova sayembekezela kuti muzicita zimene simungathe. Ndipo sationa kuti ndife ofunika cifukwa ca zimene timacita pom’tumikila. Yehova amafuna kuti tikhale odzicepetsa ndi okhulupilika. (Mika 6:8; 1 Akor. 4:2) Cimene cimam’sangalatsa kwambili si kuculuka kwa zimene timacita pom’tumikila. Amasangalala akaona kuti tili ndi makhalidwe abwino komanso tili ndi mtima wofuna kum’kondweletsa. Ndiye kodi pangakhale pomveka kufuna kucita zambili kuposa zimene Yehova amafuna kuti ticite?c Ayi ndithu! Conco, ngati simungathe kucita zambili potumikila Yehova cifukwa ca zobvuta zina, yesani kuika maganizo anu pa zimene mungathe. Mwacitsanzo, mungaphunzitseko nchito acinyamata kapena mungalimbikitseko acikulile. Mwinanso mungalimbikitse ena mwa kuwayendela, kuwaimbila foni, kapena kuwalembela meseji. Mukamadziikila zolinga zimene mungazikwanilitse, Yehova adzakuthandizani kukhala acimwemwe. Ndipo musaiwale mfundo yakuti posacedwapa, m’dziko latsopano tidzatha kutumikila Yehova m’njila zimene sitinaziganizilepo. Mfundoyi inalimbikitsa Holly, yemwe tachula m’ndime yapitayi. Anakamba kuti: “Ndimaganizila mfundo yakuti ndidzakhala kosatha. Conco, ndi thandizo la Yehova ndidzatha kumucitila zonse za mumtima mwanga.”
14. N’cianinso cina cingatilande cimwemwe?
14 Cacitatu: Kukonda zosangalatsa. Anthu ena pa soshomidiya amalimbikitsa maganizo akuti cimwemwe ceniceni cimabwela ukamacita zinthu zodzikondweletsa. Izi zapangitsa ena kumaganiza kuti munthu akamacita zimene zimam’sangalatsa, akagula katundu wa kumtima kwake, kapena akapita kumalo osiyana-siyana m’pamene angakhaledi wacimwemwe. Kucita zimenezi pakokha kulibe bvuto. Yehova anatilenga kuti tizisangalala ndi zinthu zokongola zimene analenga. Komabe, zinthu zimene anthu ambili amaganiza kuti zingawapatse cimwemwe n’zimene zimawalanda cimwemweco. Mpainiya wina, dzina lake Eva, anakamba kuti, “Ukamaika mtima wako wonse pa kudzikondweletsa sukhala wacimwemwe.” Kukonda zosangalatsa kungatipangitse kukhala osasangalala.
15. Kodi tingaphunzile ciani kwa Mfumu Solomo?
15 Zimene zinacitikila Mfumu Solomo zimveketsa bwino mfundo yakuti kukonda zosangalatsa kumagwilitsa mwala. Solomo anayesa kupeza cimwemwe mwa kucita zinthu zom’kondweletsa monga kudya cakudya cokoma, kumvetsela nyimbo zabwino, komanso kugula zinthu zonse zabwino-zabwino. Koma anakhalabe wosakhutila. Iyemwini anati: “Diso silikhuta ndi kuona, ndipo khutu silidzadza cifukwa ca kumva.” (Mlal. 1:8; 2:1-11) Zinthu zimene anthu amaganiza kuti zingawapatse cimwemwe tingaziyelekezele ndi ndalama zacinyengo. Zingaoneke ngati zaphindu, koma m’ceniceni n’zopanda pake.
16. Kodi kupatsa kungatithandize bwanji kukhalanso ndi cimwemwe? (Onaninso zithunzi.)
16 Kodi tingatani kuti tikhalenso acimwemwe? Yesu anatiphunzitsa kuti “kupatsa kumabweletsa cimwemwe cacikulu kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Mkulu wina, dzina lake Alekos, anati: “Ndimakonda kuthandiza ena powacitila zinthu zing’ono-zing’ono. Ndapeza kuti ndikamathandiza ena, sindiganizilanso kwambili zofuna zanga. Zotsatila zake n’zakuti ndimakhala wacimwemwe.” Nanga inu, n’ciani cimene mungacitileko ena? Mukaona kuti wina ali ndi cisoni, mulimbikitseni. Ngakhale kuti nthawi zina simungathetse mabvuto ake, mungamulimbikitsebe mwa kumumvetsela mosamala, kumuonetsa cifundo, komanso kumulimbikitsa kuti atulile Yehova nkhawa zake zonse. (Sal. 55:22; 68:19) Mungamukumbutsenso mfundo yakuti Yehova sanamunyanyale. (Sal. 37:28; Yes. 59:1) Ngati n’kotheka, mungadzipeleke kuti mumucitileko zinthu monga kum’konzela cakudya kapena kupita naye kokayenda. Cinanso, mungapite naye mu utumiki. Izi zidzam’thandiza kukhala wosangalala. Lolani kuti Yehova akugwilitsileni nchito polimbikitsa ena. Tikamaika zofuna za ena patsogolo, tidzakhala ndi cimwemwe ceniceni.—Miy. 11:25.
Muziika zofuna za ena patsogolo m’malo mwa zofuna zanu (Onani ndime 16)d
17. Kodi tiyenela kutani kuti tipeze cimwemwe ceniceni? (Salimo 43:4)
17 Tingakhale ndi cimwemwe ceniceni tikapitiliza kum’dziwa bwino Yehova ndi kucita zinthu zom’kondweletsa. Baibo imatitsimikizila kuti Yehova ndi ‘amene amatisangalatsa kwambili.’ (Welengani Salimo 43:4.) Cotelo, kaya tikukumana ndi mabvuto otani, sitiyenela kukhala ndi nkhawa kapena mantha. Pa cifukwa cimeneci, tiyeni tilunjike maso athu kwa Yehova, Gwelo lamuyaya la cimwemwe cathu!—Sal. 144:15.
NYIMBO 155 “Cimwemwe Cathu Camuyaya”
a Onani bokosi lakuti “Dalilani Yehova Kuti Mukhale Acimwemwe.”
b Kuti mupeze citsanzo ca zimenezi, onani nkhani ya Dennis ndi Irina Christensen m’vidiyo yakuti Ciunikilo Na. 5 ca Bungwe Lolamulila mu 2023 pa jw.org.
c Kuti mudziwe zambili, onani nkhani yakuti “Musadzipanikize, Ndipo Mudzakhala Achimwemwe” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008 ya Chichewa.
d MAU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mlongo wadzigulila zinthu zambili koma sakusangalala kwenikweni. Wapeza cimwemwe ceniceni pamene wagula maluwa oti apatse mlongo wacikulile amene akufunikila cilimbikitso.