September 4-10
EZEKIELI 42-45
Nyimbo 26 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kubwezeletsa Kulambila Koyela”: (10 min.)
Ezek. 43:10-12—Colinga ca masomphenya a kacisi amene Ezekieli anaona, cinali cofuna kulimbikitsa Ayuda anali ku ukapolo kuti alape, na kuwatsimikizila kuti kulambila koyela kudzabwezeletsedwa pa malo ake oyenelela ndi okwezeka (w99 3/1 peji 8 pala. 3; it-2 peji 1082 pala. 2)
Ezek. 44:23—Ansembe anali kudzalangiza anthu “za kusiyana kwa cinthu copatulika ndi cinthu coipitsidwa”
Ezek. 45:16—Anthu anali kudzacilikiza amene Yehova anasankha kuti azitsogolela (w99 3/1 peji 10 pala. 10)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Ezek. 43:8, 9—Kodi Aisiraeli anaipitsa bwanji dzina la Mulungu? (it-2 peji 467 pala. 4)
Ezek. 45:9, 10—Kodi Yehova amafunanji kwa anthu ofuna ciyanjo cake? (it-2 peji 140)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Ezek. 44:1-9
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani na kukambilana mavidiyo payokha-payokha.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“N’cifukwa Ciani Kulambila Koyela Kuli Kofunika?”: (15 min.) Kukambilana.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 17 mapa. 10-18
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 115 na Pemphelo